Numeri 24:1-25

  • Ndakatulo yachitatu ya Balamu (1-11)

  • Ndakatulo ya 4 ya Balamu (12-25)

24  Balamu ataona kuti Yehova akufuna* kudalitsa Aisiraeli, sanapitenso kukafunafuna njira yoti awalodzere,+ mʼmalomwake anayangʼana kuchipululu. 2  Balamu atakweza maso ake nʼkuona Aisiraeli ali mʼmisasa mogwirizana ndi mafuko awo,+ mzimu wa Mulungu unafika pa iye.+ 3  Kenako analankhula mwa ndakatulo kuti:+ “Mawu a Balamu mwana wa Beori,Mawu a mwamuna amene maso ake atseguka,  4  Mawu a munthu amene wamva mawu a Mulungu,Amene waona masomphenya a Wamphamvuyonse,Amene wagwada pansi, maso ake ali otsegula. Mawu ake akuti:+  5  Akongolerenji matenti ako, iwe Yakobo,Komanso malo ako okhala, iwe Isiraeli!+  6  Andanda kukafika kutali ngati zigwa,*+Ngati minda mʼmphepete mwa mtsinje.Ngati mitengo ya aloye imene Yehova anadzala,Ngati mikungudza mʼmbali mwa madzi.  7  Madzi odzaza mitsuko yake iwiri akutayikirabe pansi,Ndipo mbewu* yake yadzalidwa mʼmbali mwa madzi ambiri.+ Mfumu yakenso+ idzakhala yamphamvu kuposa Agagi,+Ndipo ufumu wake udzakwezedwa.+  8  Mulungu akumutulutsa mu Iguputo.Iye ali ngati nyanga za ngʼombe yamʼtchire yamphongo. Adzawononga anthu a mitundu ina, amene akumupondereza,+Adzakungudza* mafupa awo, ndipo adzawaswa ndi mivi yake.  9  Iye wagwada pansi, wagona pansi ngati mkango,Ngati mkango, ndani angayese kumʼdzutsa? Amene akudalitsa iwe adzadalitsidwa,Ndipo amene akukutemberera, adzatembereredwa.”+ 10  Kenako Balaki anapsera mtima Balamu. Ndiyeno Balaki anawomba mʼmanja mokwiya nʼkuuza Balamu kuti: “Ndinakuitana kuti udzatemberere adani anga,+ koma iwe wawadalitsa kwambiri maulendo atatu onsewa. 11  Nyamuka pompano uzipita kwanu. Ine ndimafuna ndikupatse mphoto,+ koma taona! Yehova wakulepheretsa kulandira mphoto.” 12  Balamu anayankha Balaki kuti: “Kodi anthu amene munawatuma aja sindinawauze kuti, 13  ‘Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yodzaza siliva ndi golide, sindingachite chilichonse chimene ndikufuna,* kaya chabwino kapena choipa, chosemphana ndi zimene Yehova walamula? Kodi sindinanene kuti ndikalankhula zokhazo zimene Yehova akandiuzeʼ?+ 14  Tsopano ndikupita kwa anthu a mtundu wanga. Koma tabwerani kuti ndikuuzeni zimene anthuwa adzachite kwa anthu anu mʼtsogolo.” 15  Kenako analankhula mwa ndakatulo kuti:+ “Mawu a Balamu mwana wa Beori,Mawu a mwamuna amene maso ake ndi otsegula,+ 16  Mawu a munthu amene wamva mawu a Mulungu,Amene akudziwa Wamʼmwambamwamba,Anaona masomphenya a Wamphamvuyonse,Atagwada pansi, maso ake ali otsegula. Mawu ake akuti: 17  Ndidzamuona, koma osati panopa;Ndidzamupenya, koma osati posachedwa. Nyenyezi+ idzatuluka mwa Yakobo,Ndodo yachifumu+ idzatuluka mu Isiraeli.+ Ndipo iye adzaphwanyadi chipumi cha Mowabu+Ndi mitu ya asilikali onse ankhanza. 18  Edomu adzalandidwa,+Ndithu Seiri+ adzalandidwa ndi adani ake,+Pamene Isiraeli akuonetsa kulimba mtima kwake. 19  Wina adzatuluka mwa Yakobo kukagonjetsa,+Ndipo adzawononga aliyense amene wapulumuka mumzindamo.” 20  Balamu ataona Amaleki, anapitiriza mawu ake a ndakatulo kuti: “Amaleki anali woyamba pa anthu a mitundu ina,*+Koma mapeto ake adzawonongedwa.”+ 21  Ataona Akeni+ anapitiriza kulankhula mwa ndakatulo kuti: “Mumakhala motetezeka, malo anu okhala ali pathanthwe. 22  Koma Kayini* adzawotchedwa ndi moto. Kodi padzatenga nthawi yayitali bwanji Asuri asanakugwire nʼkupita nawe kudziko lina?” 23  Anapitiriza kulankhula mwa ndakatulo kuti: “Mayo ine! Ndani adzapulumuke Mulungu akadzachita zimenezi? 24  Sitima zidzafika kuchokera kudoko la Kitimu,+Ndipo iwo adzazunza Asuri,+Adzazunza Ebere. Koma iyenso adzawonongedwa kotheratu.” 25  Kenako Balamu+ ananyamuka nʼkubwerera kwawo. Nayenso Balaki anapita kwawo.

Mawu a M'munsi

^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ataona kuti ndi zabwino mʼmaso mwa Yehova.”
^ Kapena kuti, “makhwawa.”
^ Kapena kuti, “mbadwa.”
^ “Kukungudza” ndi kuchotseratu mnofu wonse pafupa tikamadya nyama.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chochokera mumtima mwanga.”
^ Kutanthauza kuti anali oyamba kuukira Aisiraeli atatuluka mʼdziko la Iguputo.
^ “Kayini” akuimira fuko la “Akeni.”