Miyambo 21:1-31

  • Yehova amatsogolera mtima wa mfumu (1)

  • Kuchita zinthu zachilungamo nʼkwabwino kuposa kupereka nsembe (3)

  • Khama limapindulitsa (5)

  • Amene samvetsera munthu wonyozeka nayenso sadzamvetseredwa (13)

  • Palibe nzeru zotsutsana ndi Yehova (30)

21  Mtima wa mfumu uli ngati mitsinje yamadzi mʼdzanja la Yehova.+ Amaupititsa kulikonse kumene iye akufuna.+  2  Njira zonse za munthu zimaoneka zabwino kwa iye,+Koma Yehova amafufuza mitima.*+  3  Kuchita zinthu zoyenera komanso zachilungamoKumasangalatsa kwambiri Yehova kuposa nsembe.+  4  Maso odzikweza komanso mtima wonyadaZili ngati nyale imene imatsogolera anthu oipa, koma zimenezi ndi tchimo.+  5  Mapulani a munthu wakhama amamuthandiza kuti zinthu zimuyendere bwino,*+Koma onse amene amachita zinthu mopupuluma amasauka.+  6  Kupeza chuma pogwiritsa ntchito lilime lonamaKuli ngati nkhungu imene imachoka mofulumira komanso msampha wakupha.*+  7  Zinthu zachiwawa zimene anthu oipa amachita nʼzimene zidzawawononge,+Chifukwa amakana kuchita zinthu mwachilungamo.  8  Njira ya munthu wochimwa imakhala yokhotakhota,Koma zochita za munthu wolungama ndi zowongoka.+  9  Ndi bwino kukhala pakona ya denga la nyumbaKusiyana ndi kukhala mʼnyumba limodzi ndi mkazi wolongolola.*+ 10  Munthu woipa amalakalaka zoipa,+Ndipo mnzake samukomera mtima.+ 11  Munthu wonyoza akapatsidwa chilango, wosadziwa zinthu amakhala wanzeru,Ndipo munthu wanzeru akaphunzira zinthu zambiri, amadziwa zinthu.*+ 12  Mulungu amene ndi wolungama amayangʼana nyumba ya munthu woipa.Amagwetsa anthu oipa kuti akumane ndi tsoka.+ 13  Aliyense amene amatseka khutu lake kuti asamve kudandaula kwa munthu wonyozeka,Nayenso adzaitana koma sadzayankhidwa.+ 14  Mphatso yoperekedwa mwachinsinsi imathetsa mkwiyo,+Ndipo chiphuphu choperekedwa mwamseri* chimathetsa ukali waukulu. 15  Wolungama amasangalala akamachita chilungamo,+Koma anthu ochita zoipa amadana ndi chilungamo. 16  Munthu amene wasochera nʼkusiya kuchita zinthu mozindikiraAdzapumula mʼgulu la anthu akufa.+ 17  Munthu amene amakonda zosangalatsa adzasauka.+Amene amakonda vinyo ndi mafuta sadzalemera. 18  Munthu woipa ndi dipo la munthu wolungama,Ndipo munthu wochita zachinyengo adzatengedwa mʼmalo mwa anthu owongoka mtima.+ 19  Ndi bwino kukhala mʼchipululuKusiyana ndi kukhala ndi mkazi wolongolola* komanso wosachedwa kukwiya.+ 20  Chuma chamtengo wapatali komanso mafuta zimapezeka mʼnyumba ya munthu wanzeru,+Koma munthu wopusa amasakaza* zinthu zimene ali nazo.+ 21  Amene akufunafuna chilungamo ndiponso chikondi chokhulupirikaAdzapeza moyo, chilungamo ndi ulemerero.+ 22  Munthu wanzeru amagonjetsa* mzinda wa anthu amphamvu,Ndipo amawononga mpanda wolimba umene amadalira.+ 23  Amene amateteza pakamwa pake komanso lilime lakeAmapewa mavuto.+ 24  Munthu wochita zinthu modzikuza amene saganizira zotsatira zake ndi amene mumamutiNdi munthu wonyada komanso amene amakonda kudzionetsera ndiponso kudzitamandira.+ 25  Zinthu zimene munthu waulesi amalakalaka zidzamupha,Chifukwa manja ake amakana kugwira ntchito.+ 26  Tsiku lonse amalakalaka chinachake mwadyera,Koma munthu wolungama amapereka, saumira chilichonse.+ 27  Nsembe ya munthu woipa ndi yonyansa.+ Ndiye kuli bwanji akaipereka ndi zolinga zoipa!* 28  Mboni yonena mabodza idzawonongedwa,+Koma munthu amene amamvetsera adzapereka umboni wa zinthu zimene anamva ndipo zidzamuyendera bwino.* 29  Munthu woipa amadzionetsa ngati wolimba mtima,+Koma wolungama amasankha njira yoyenera kuyenda.+ 30  Palibe nzeru kapena kuzindikira, kapena malangizo amene angalepheretse zimene Yehova amafuna.+ 31  Hatchi amaiphunzitsa pokonzekera tsiku la nkhondo,+Koma Yehova ndi amene amapulumutsa.+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “zolinga.”
^ Kapena kuti, “zinthu zimupindulire.”
^ Mabaibulo ena amati, “mofulumira kwa amene akufunafuna imfa.”
^ Kapena kuti, “wokonda kudandaula.”
^ Kapena kuti, “amadziwa zoyenera kuchita.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chiphuphu chobisidwa pachovala.”
^ Kapena kuti, “wokonda kudandaula.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amameza.”
^ Kapena kuti, “amakwera mpanda wa.”
^ Kapena kuti, “limodzi ndi khalidwe lochititsa manyazi.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “adzalankhula kwamuyaya.”