Miyambo 13:1-25

  • Anthu amene amapempha malangizo amakhala ndi nzeru (10)

  • Chimene umayembekezera chikalephereka, mtima umadwala (12)

  • Nthumwi yokhulupirika imachiritsa (17)

  • Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru (20)

  • Chilango chimasonyeza chikondi (24)

13  Mwana wanzeru amalandira malangizo* ochokera kwa bambo ake,+Koma wonyoza samvera akadzudzulidwa.*+  2  Munthu adzadya zinthu zabwino kuchokera pa zipatso zapakamwa pake,+Koma anthu achinyengo amalakalaka kuchita zachiwawa.  3  Amene amayangʼanira pakamwa pake* amateteza moyo wake,+Koma amene amatsegula kwambiri pakamwa pake adzawonongeka.+  4  Waulesi amalakalaka zinthu, chonsecho alibe chilichonse.+Koma munthu wakhama zinthu zidzamuyendera bwino.*+  5  Wolungama amadana ndi mabodza,+Koma zochita za munthu woipa zimabweretsa manyazi ndi kunyozeka.  6  Chilungamo chimateteza munthu wosalakwa,+Koma kuchita zoipa kumachititsa kuti wochimwa awonongeke.  7  Pali munthu amene amadzionetsa ngati wolemera koma chonsecho alibe chilichonse.+Pali munthu winanso amene amadzionetsa ngati wosauka koma ali ndi chuma chambiri.  8  Chuma chimawombola moyo wa munthu,+Koma anthu osauka saopsezedwa* nʼkomwe.+  9  Kuwala kwa nyale ya anthu olungama kukuwonjezeka kwambiri.*+Koma nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.+ 10  Kudzikuza kumangoyambitsa mikangano basi,+Koma anthu amene amapempha malangizo* amakhala ndi nzeru.+ 11  Chuma chimene munthu amachipeza mofulumira* sichichedwa kutha,+Koma chuma cha munthu amene wachipeza pangʼonopangʼono* chidzawonjezeka. 12  Chinthu chimene umayembekezera chikalephereka, mtima umadwala.+Koma chomwe umalakalaka chikachitika, chimakhala ngati mtengo wa moyo.+ 13  Aliyense amene safuna kutsatira malangizo, adzakumana ndi mavuto chifukwa cha zochita zakezo,+Koma munthu amene amamvera malamulo adzalandira mphoto.+ 14  Zimene munthu wanzeru amaphunzitsa* zimapereka moyo,+Chifukwa zimapulumutsa munthu kumisampha ya imfa. 15  Munthu wozindikira kwambiri, anthu amamukomera mtima,Koma anthu achinyengo moyo wawo umakhala wodzaza ndi mavuto. 16  Munthu wochenjera amadziwa zimene akuchita,+Koma wopusa amaonetsa uchitsiru wake wonse.+ 17  Munthu woipa wobweretsa uthenga amakumana ndi mavuto,+Koma nthumwi yokhulupirika imachiritsa.+ 18  Aliyense amene amanyalanyaza malangizo* amasauka ndipo amanyozeka,Koma amene amamvera akadzudzulidwa adzalemekezedwa.+ 19  Zimene munthu amalakalaka zikakwaniritsidwa amasangalala.+Koma opusa amadana ndi zoti asiye zinthu zoipa.+ 20  Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru,+Koma amene amachita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.+ 21  Tsoka limatsatira ochimwa,+Koma anthu olungama zinthu zimawayendera bwino.+ 22  Munthu wabwino amasiyira cholowa zidzukulu zake,Koma chuma cha munthu wochimwa chidzasungidwa kuti chidzakhale cha munthu wolungama.+ 23  Munda wa munthu wosauka akaulima umatulutsa chakudya chochuluka,Koma chingathe kutengedwa* ndi anthu opanda chilungamo. 24  Munthu amene sakwapula* mwana wake ndiye kuti akudana naye,+Koma amene amamukonda salephera* kumupatsa chilango.+ 25  Wolungama amadya nʼkukhuta,+Koma mimba za anthu oipa zimakhala zopanda kanthu.+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “akalangizidwa.”
^ Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
^ Kapena kuti, “zimene amalankhula.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “adzanenepa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “sadzudzulidwa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kukusangalala.”
^ Kapena kuti, “amene amakhala pamodzi nʼkumakambirana.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wachisonkhanitsa ndi manja ake.”
^ Kapena kuti, “mʼnjira zachinyengo.”
^ Kapena kuti, “Chilamulo cha munthu wanzeru.”
^ Kapena kuti, “akadzudzulidwa.”
^ Kapena kuti, “angathe kuwonongedwa.”
^ Kapena kuti, “sapereka chilango kwa.”
^ Mabaibulo ena amati, “sazengereza.”