Salimo 116:1-19

  • Nyimbo yoyamikira

    • “Yehova ndidzamubwezera chiyani?” (12)

    • “Ndidzamwa zamʼkapu yachipulumutso” (13)

    • “Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova” (14, 18)

    • Imfa ya anthu okhulupirika ndi yopweteka kwambiri (15)

116  Ndimakonda YehovaChifukwa amamva mawu anga komanso kuchonderera kwanga kopempha thandizo.+  2  Amatchera khutu lake nʼkundimvetsera,*+Ndipo ndidzaitanira pa iye moyo wanga wonse.*  3  Zingwe za imfa zinandikulunga.Ndinkangomva ngati ndatsala pangʼono kufa.+ Ndinavutika chifukwa cha nkhawa komanso chisoni.+  4  Koma ndinaitana pa dzina la Yehova kuti:+ “Inu Yehova, ndipulumutseni!”  5  Yehova ndi wokoma mtima* komanso wolungama.+Mulungu wathu ndi wachifundo.+  6  Yehova amateteza anthu osadziwa zambiri.+ Ndinafooka chifukwa cha nkhawa koma iye anandipulumutsa.  7  Moyo wanga upumulenso,Chifukwa Yehova wandichitira zinthu mokoma mtima.  8  Inu mwandipulumutsa ku imfa,Mwapukuta misozi yanga ndipo mwateteza phazi langa kuti lisapunthwe.+  9  Ndidzayenda pamaso pa Yehova mʼdziko la anthu amoyo. 10  Ndinali ndi chikhulupiriro, nʼchifukwa chake ndinalankhula.+Ndinavutika kwambiri. 11  Nditapanikizika ndinati: “Munthu aliyense ndi wabodza.”+ 12  Yehova ndidzamubwezera chiyaniPa zabwino zonse zimene wandichitira? 13  Ndidzamwa zamʼkapu yachipulumutso,*Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova. 14  Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,Pamaso pa anthu ake onse.+ 15  Mʼmaso mwa YehovaImfa ya anthu ake okhulupirika ndi yopweteka kwambiri.*+ 16  Ndikukupemphani, inu Yehova,Chifukwa ine ndi mtumiki wanu. Ndine mtumiki wanu, mwana wa kapolo wanu wamkazi. Mwamasula zingwe zimene anandimanga nazo.+ 17  Ndidzapereka nsembe zoyamikira kwa inu,+Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova. 18  Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+Pamaso pa anthu ake onse,+ 19  Mʼmabwalo a nyumba ya Yehova,+Pakati pa iwe Yerusalemu. Tamandani Ya!*+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “amawerama kuti andimvetsere.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmasiku anga.”
^ Kapena kuti, “ndi wachisomo.”
^ Kapena kuti, “yachipulumutso chachikulu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi nkhani yaikulu.”
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.