Mipukutu ya Baibo
Kuŵelenga Mpukutu Wamakedzana Wakupsa na Moto
Mu 1970, akatswili ofukula zinthu zakale, anapeza mpukutu wakupsa na moto ku Ein Gedi, m’dziko la Israel. Poseŵenzetsa makina amakono ounikila zinthu, akatswili akwanitsa kuŵelenga mpukutuwu. Kodi n’ciani cimene anapeza pambuyo pouŵelenga?
Baibulo Siinawole
Olemba ndi okopela Baibulo aluso anali kuseŵenzetsa gumbwa ndi zikumba polemba uthenga wa m’Baibulo. Kodi mipukutu yakale ya Baibulo masauzande ambili inatetezeka bwanji mpaka masiku ano?

