Onani zimene zilipo

Onani menyu yaciŵili

Mboni za Yehova

Cinyanja

Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupilila Yesu?

Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupilila Yesu?

Inde. Timakhulupilila Yesu amene ananena kuti: “Ine ndine njila, coonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzela mwa ine.” (Yohane 14:6) Ndipo timakhulupilila kuti Yesu anabwela padziko lapansi kucokela kumwamba ndi kupeleka moyo wake monga nsembe ya dipo. (Mateyu 20:28) Imfa yake inapangitsa kuti anthu amene amakhulupilila iye akhale ndi ciyembekezo codzalandila moyo wosatha. (Yohane 3:16) Ndiponso timakhulupilila kuti Yesu tsopano akulamulila monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu, umene udzabweletsa mtendele padziko lonse posacedwapa. (Chivumbulutso 11:15) Koma timakhulupilila kuti Yesu si wofanana ndi Mulungu cifukwa cakuti iye anati: “Atate ndi wamkulu kuposa ine.” (Yohane 14:28) Conco, sitilambila Yesu cifukwa cakuti timakhulupilila kuti iye si Mulungu Wamphamvuyonse.