Onani m’maganizo mwanu nkhani za m’Baibulo mwa kugwilitsila nchito zomvetsela zokhala ndi congo cinacake, nyimbo ndi wosimba wake. Zimenezi mungazitenge pa webusaiti yathu. Mavidiyo a zinenelo za manja naonso alipo.

Sankhani cinenelo pa bokosi la zinenelo, ndiyeno dinizani pa Funani kuti muone maseŵelo a m’Baibulo amene alipo m’cinenelo cimeneco. Lembani mbali ya mutu kapena dzina la buku la m’Baibulo kuti muone pamene mufunika kuŵelenga m’Baibulo.