Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

 Phunzilo 3

Kodi Uthenga Wabwino Ni Wocokeladi kwa Mulungu?

Kodi Uthenga Wabwino Ni Wocokeladi kwa Mulungu?

1. Kodi Ndani Analemba Baibo?

Uthenga wabwino wakuti anthu adzakhala ndi moyo wamuyaya padziko lapansi umapezeka m’Baibo. (Salimo 37:29) Baibo yonse ili ndi mabuku ang’ono-ang’ono okwana 66. Mulungu anagwilitsila nchito amuna pafupi-fupi 40 kulemba Baibo. Mabuku asanu oyambilila analembedwa ndi Mose pafupi-fupi zaka 3,500 zapitazo. Buku lotsilizila linalembedwa ndi mtumwi Yohane pafupi-fupi zaka 1,900 zapitazo. Kodi olemba Baibo analemba maganizo a ndani? Mulungu anagwilitsila nchito mzimu woyela kukamba ndi anthu amene analemba Baibo. (2 Samueli 23:2) Iwo analemba maganizo a Mulungu, osati maganizo ao. Mwa ici, Yehova ndiye analemba Baibo.—Ŵelengani 2 Timoteyo 3:16; 2 Petulo 1:20, 21.

2. Kodi Tingatsimikizile Bwanji Kuti Baibo Imakamba Zoona?

Timadziŵa kuti Baibo ni yocokela kwa Mulungu cifukwa imakamba zoona ndiponso mwatsatane-tsane pa zinthu zimene zidzacitika kutsogolo. Palibe munthu amene angacite zimenezi. (Yoswa 23:14) Mulungu Wamphamvuyonse yekha ndi amene angadziŵiletu zimene zidzacitika kwa anthu kutsogolo.—Ŵelengani Yesaya 42:9; 46:10.

Timayembekezele buku locokela kwa Mulungu kukhala lapadela, ndipo ni mmene Baibo ilili. Mabaibo mabiliyoni ambili afalitsidwa m’zinenelo zambili. Ngakhale kuti inalembedwa kale kwambili, Baibo imagwilizana ndi sayansi. Ndiponso, olemba ake okwana 40 sanalembe zotsutsana. * Komanso, zimene Baibo imakamba za cikondi zimacokela kokha kwa Mulungu woona amene ni Mulungu wacikondi. Baibo ilinso ndi mphamvu yokwanitsa kusintha makhalidwe a anthu kuti akhale abwino. Mfundo zimenezi zimatsimikizila anthu mamiliyoni kuti Baibo ni Mau a Mulungu.—Ŵelengani 1 Atesalonika 2:13.

 3. Kodi Baibo imatiuza za ciani?

Baibo imatiuza za uthenga wabwino wakuti Mulungu ali ndi colinga cabwino kwa anthu ake. Malemba amafotokoza mmene munthu paciyambi peni-peni anataila mwai wokhala m’paladaiso padziko lapansi, ndi mmene Mulungu adzabwezeletsela paladaiso ameneyu.—Ŵelengani Chivumbulutso 21:4, 5.

Mau a Mulungu alinso ndi malamulo, mfundo, ndi malangizo. Kuonjezela apo, Baibo imafotokoza mbili yakale ya mmene Mulungu anali kucitila ndi anthu, ndiponso mbili yakale imeneyi imatidziŵitsa kuti Mulungu ndi wotani. Conco, Baibo ingakuthandizeni kuti mudziŵe Mulungu. Imafotokoza mmene mungakhalile bwenzi lake.—Ŵelengani Salimo 19:7, 11; Yakobo 2:23; 4:8.

4. Kodi mungacite ciani kuti muimvetsetse Baibo?

Kabuku aka kadzakuthandizani kuti muimvetsetse Baibo mwa kugwilitsila nchito njila imene Yesu nayenso anagwilitsila nchito. Iye anali kuchula Malemba kaŵili-kaŵili ndi kufotokoza “tanthauzo la Malemba.”—Ŵelengani Luka 24:27, 45.

Pali zinthu zocepa cabe zimene zili zocititsa cidwi mofanana ndi uthenga wabwino wocokela kwa Mulungu. Ngakhale n’conco, anthu ena alibe nao cidwi, ndipo ena amakhumudwa akamauzidwa uthenga umenewu. Koma musataye mtima. Mufunika kudziŵa Mulungu kuti mukhale ndi ciyembekezo ca moyo wosatha.—Ŵelengani Yohane 17:3.

 

^ par. 7 Onani kabuku kakuti Buku la Anthu Onse.