1. N’cifukwa ciani cikwati ca lamulo n’cofunika kuti banja likhale lacimwemwe?

Uthenga wabwino umacokela kwa Yehova, amene ndi Mulungu wacimwemwe. Amafuna kuti mabanja azikhala acimwemwe. (1 Timoteyo 1:11) Iye ndi amene anayambitsa cikwati. Cikwati ca lamulo n’cofunika kuti banja likhale lacimwemwe. Cikwati cimeneci cimathandiza kuti ana aleledwe bwino ndi kuti akhale otetezeka.

Kodi Mulungu amaciona bwanji cikwati? Iye amafuna kuti mwamuna ndi mkazi akakwatilana azikhala pamodzi kwa moyo wao wonse. Akristu ayenela kutsatila malamulo okhudza kulembetsa cikwati. (Luka 2:1, 4, 5) Yehova amafuna kuti mwamuna ndi mkazi azikhala okhulupilika kwa wina ndi mnzake. (Aheberi 13:4) Iye amadana ndi kutsiliza cikwati. (Malaki 2:16) Koma amalola Akristu kutsiliza cikwati ndi kukwatilanso ngati wina wa m’cikwati cimeneco wacita cigololo.Ŵelengani Mateyu 19:3-6, 9.

2 Kodi mwamuna ndi mkazi ayenela kucitilana bwanji zinthu?

Yehova analenga amuna ndi akazi kuti azithandizana m’cikwati. (Genesis 2:18) Monga mutu wa banja, mwamuna ayenela kusamalila zosoŵa za kuthupi za banja lake ndi kutsogolela powaphunzitsa za Mulungu. Ayenela kudzimana poonetsa cikondi kwa mkazi wake. Mwamuna ndi mkazi ayenela kuonetsana cikondi ndi ulemu. Popeza kuti amuna ndi akazi onse ndi opanda ungwilo, afunika kuphunzila kukhala ndi mtima wokhululuka kuti banja likhale lacimwemwe.Ŵelengani Aefeso 4:31, 32; 5:22-25, 33; 1 Petulo 3:7.

3. Kodi muyenela kuthawa m’cikwati cifukwa ca mavuto?

Ngati mukumana ndi mavuto m’cikwati canu, nonse aŵili muyenela kuyesa-yesa kucitilana zinthu mwacikondi. (1 Akorinto  13:4, 5) Mau a Mulungu savomeleza kupatukana monga njila yothetsela mavuto amene kaŵili-kaŵili amapezeka m’banja.Ŵelengani 1 Akorinto 7:10-13.

4. Ana inu, kodi Mulungu amakufunilani ciani?

Yehova amafuna kuti muzikhala acimwemwe. Iye anakupatsani malangizo abwino kwambili a mmene mungakhalile okondwela ndi ucicepele wanu. Amafuna kuti mupindule ndi nzelu ndi cidziŵitso cimene makolo anu ali naco. (Akolose 3:20) Yehova nayenso amafuna kuti mukhale ndi cimwemwe cimene cimabwela cifukwa cocita zimene Mlengi wanu ndi Mwana wake amafuna.Ŵelengani Mlaliki 11:9–12:1; Mateyu 19:13-15; 21:15, 16.

5. Makolo, kodi ana anu angakhale bwanji acimwemwe?

Muyenela kulimbikila nchito kuti muwapezele cakudya, malo ogona ndi zovala. (1 Timoteyo 5:8) Koma kuti ana anu akhale acimwemwe, inunso mufunika kuwaphunzitsa kukonda Mulungu ndi kuphunzila kwa iye. (Aefeso 6:4) Citsanzo canu ca kukonda Mulungu cingakhudze kwambili mitima ya ana anu. Ngati malangizo anu amacokela m’Mau a Mulungu, adzathandiza ana anu kuti akhale ndi maganizo abwino.Ŵelengani Deuteronomo 6:4-7; Miyambo 22:6.

Ana amapindula kwambili ngati muwalimbikitsa ndi kuwayamikila. Amafunikilanso kuwalangiza ndi kuwapatsa cilango. Kucita zimenezi kumawateteza ku makhalidwe amene angawalande cimwemwe. (Miyambo 22:15) Koma cilango siciyenela kupelekedwa mwankhanza.Ŵelengani Akolose 3:21.

Mboni za Yehova zimafalitsa mabuku angapo amene analembedwa maka-maka kuti athandize makolo ndi ana. Mfundo zimene zili m’mabuku amenewa n’zocokela m’Baibo.Ŵelengani Salimo 19:7, 11.