Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Uthenga Wabwino Wocokela Kwa Mulungu

Kodi uthenga wabwino wocokela kwa Mulungu n’ciani? N’cifukwa ciani tiyenela kuukhulupilila? Kabuku aka kayankha mafunso amene anthu ambili amafunsa.

Mmene Kabuku aka Kangakuthandizileni

Kabuku aka kadzakuthandizani kukhala ndi mtima wokonda kuphunzila Mau a Mulungu, Baibo. Onani mmene mungapezele lemba m’Baibo yanu.

Kodi Uthenga Wabwino n’Ciani?

Phunzilani za uthenga wocokela kwa Mulungu, cifukwa cake uli wofunika kwambili, ndiponso zimene muyenela kucita.

Kodi Mulungu Ndani?

Kodi Mulungu ali ndi dzina ndipo kodi amasamala za ife?

Kodi Uthenga Wabwino Ni Wocokeladi kwa Mulungu?

Kodi tingatsimikizile bwanji kuti baibo imakamba zoona?

Kodi Yesu Kristu Ndani?

Phunzilani mmene moyo wa Yesu unayambila, cifukwa cake anabwela padziko lapansi, ndi zimene akucita tsopano.

Kodi Mulungu Ali Nalo Colinga Canji Dziko Lapansi?

Baibo imafotokoza cifukwa cake Mulungu analenga dziko, mmene mavuto adzathela, ndi mmene dziko lidzakhalila mtsogolo, komanso amene adzakhala mmenemo.

Kodi Tili ndi Ciyembekezo Canji Ponena za Akufa?

Kodi n’ciani cimacitika tikafa? Kodi okondedwa athu akufa tidzawaonanso?

Kodi Ufumu wa Mulungu n’Ciani?

Kodi Mfumu ya ufumu wa Mulungu ndani? Nanga udzacita ciani?

N’cifukwa Ciani Mulungu Amalolela Kuti Anthu Azivutika?

Kodi mavuto anayamba bwanji? Nanga n’cifukwa ciani Mulungu walola mavuto mpaka lelo? Kodi mavuto adzatha?

Mungacite Ciani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?

Yehova Mulungu wacimwemwe amafuna kuti mabanja akhale acimwemwe. Pezani mfundo zothandiza kwa amuna, akazi, makolo, ndi ana.

Kodi Kulambila Koona Mungakudziŵe Bwanji?

Kodi pali cipembedzo coona cimodzi cabe? Onani mfundo zisanu zodziŵikitsa kulambila koona.

Kodi Mfundo za m’Baibo Zimatithandiza Bwanji?

Yesu anafotokoza cifukwa cake timafunikila citsogozo ndi mfundo za m’Baibo ziŵili zofunika kwambili.

Kodi Mungamuyandikile Bwanji Mulungu?

Dziŵani ngati kuti Mulungu amamva mapemphelo onse, kuti tiyenela kupemphela bwanji, ndi zina zimene tingacite kuti timuyandikile Mulungu.

Kodi Uthenga Wabwino Wonena za Cipembedzo ndi Uti?

Kodi padzakalako nthawi pamene anthu onse adzagwilizana pa kulambila Mulungu woona mmodzi yekha?

N’cifukwa Ciani Mulungu Ali ndi Gulu?

Baibo imatiuza cifukwa cake Akristu oona ali gulu ndiponso kuti ndi olinganizika.

N’cifukwa Ciani Muyenela Kupitilizabe Kuphunzila za Yehova?

Kodi kudziŵa kwanu Mulungu ndi Mau ake kungathandize bwanji ena? Kodi ndi ubwenzi wanji umene mungakhale nao ndi Mulungu?