Onani zimene zilipo

Kodi Mufuna Kudziŵa Mayankho Azoona pa Mafunso Aya?

Kodi Mufuna Kudziŵa Mayankho Azoona pa Mafunso Aya?

Aya ni mafunso ofunika kwambili amene anthu amakonda kufunsa. Kapena na imwe munadzifunsapo mafunso akuti:

  • Kodi zoona Mulungu amasamala za ife?
  • Kodi nkhondo na mavuto zidzasila?
  • Kodi munthu akafa, cimacitika kwa iye ni ciyani?
  • Kodi anthu amene anafa adzauka?
  • Ningapemphele bwanji kuti Mulungu azinimvela?
  • Ningapeze bwanji cimwemwe mu moyo wanga?

Kodi mayankho a mafunso amene aya mungayapeze kuti? Mukayenda ku malaibulale kapena ku mashopu ogulitsa mabuku, mungapeze mabuku ambili amene angaoneke monga ali na mayankho. Koma mabuku amenewo kambili amatsutsana. Ena amakhala othandiza kwa nthawi ifupi cabe, koma pambuyo pake amasila nchito ndipo amalemba ena.

Koma, pali buku imodzi imene ili na mayankho omveka. Buku imeneyi imakamba vazoona. Yesu anapemphela kwa Mulungu kuti: “Mau anu ndi coonadi.” (Yohane 17:17) Masiku ano timadziŵa kuti Mau amenewo ni Baibo. Pamapeji okonkhapo, mudzapeza mayankho omveka ndiponso azoona a mafunso amene ali pamwamba apa.

Kodi Zoona Mulungu Amasamala za ife?

Mwamuna wozungulilidwa ndi anthu

CIMENE ANTHU AMAFUNSILA FUNSO IMENEYI: Mu dziko imene tikhalamo, anthu ambili amacitila anzawo nkhanza na vinthu voipa. Machechi ambili amaphunzitsa kuti Mulungu ni wamene amaleta mavuto ambili amene timakumana nawo.

ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA: Mulungu si wamene amacititsa vinthu voipa. Yobu 34:10 imakamba kuti: “Nkutali ndi Mulungu kucita coipa, ndi Wamphamvuyonse kucita chosalungama.” Mulungu ni wacikondi ndipo afuna kuticitila vinthu vabwino. Ndiye cifukwa cake Yesu anatiphunzitsa kupemphela kuti: “Atate wathu wakumwamba,…ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kucitidwe, monga kumwamba comweco pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Mulungu amasamala kwambili za ife cakuti wacita vinthu vikulu kuti akwanilitse cifunilo cake.—Yohane 3:16.

Ŵelengani Genesis 1:26-28; Yakobo 1:13; na 1 Petro 5:6, 7.

Kodi Nkhondo na Mavuto Zidzasila?

Asilikali

CIMENE ANTHU AMAFUNSILA FUNSO IMENEYI: Nkhondo zikupitiliza kupha anthu ambili. Ndipo tonse mavuto timakumana nawo.

ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA: Mulungu anakambilatu nthawi imene adzabweletsa mtendele padziko lonse. Mu Ufumu wake, umene ni boma yakumwamba, anthu ‘sadzaphunzilanso nkhondo.’ Koma ‘adzasula malupanga awo akhale zolimila.’ (Yesaya 2:4) Mulungu adzacotsa voipa na mavuto onse. Baibo imalonjeza kuti: “[Mulungu] adzawapukutila misozi yonse kuicotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulila, kapena cowawitsa; zoyambazo [zoipa na mavuto] zapita.”—Cibvumbulutso 21:3, 4.

Ŵelengani Salmo 37:10, 11; 46:9; na Mika 4:1-4.

Kodi Munthu Akafa, Cimacitika kwa Iye ni Ciyani?

Manda

CIMENE ANTHU AMAFUNSILA FUNSO IMENEYI: Machechi ambili amaphunzitsa kuti munthu akafa, mzimu wake umapitiliza kukhala na moyo. Ena amakhulupilila kuti munthu amene anafa angakuukile ciŵanda, kapena kuti Mulungu amaweluza anthu kuti akapse mu mulilo [moto] wa ku helo.

ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA: Munthu akafa, sakhalanso na moyo kwina. Mlaliki 9:5 imakamba kuti: “Akufa sadziŵa kanthu bi.” Popeza akufa sadziŵa kanthu, ndipo samvela kapena kucita ciliconse, iwo sangacitile anthu amoyo voipa kapena kuŵathandiza.—Salmo 146:3, 4.

Ŵelengani Genesis 3:19 na Mlaliki 9:6, 10.

Kodi Anthu Amene Anafa Adzauka?

Mwana alila wacibululu amene anafa

CIMENE ANTHU AMAFUNSILA FUNSO IMENEYI: Tonse timafuna moyo ndipo timafuna kukondwela pamodzi na anthu amene timakonda. Mwacibadwa timafuna kudzaonananso na acibanja athu kapena anzathu amene anafa.

ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA: Anthu ambili amene anafa adzauka. Yesu analonjeza kuti anthu amene ali mu manda adzauka. (Yohane 5:28, 29) Mogwilizana na cifunilo ca Mulungu ca poyamba, anthu amene adzauka adzakhala na mwayi wokhala mu paladaiso padziko lapansi. (Luka 23:43) Panthawi imeneyo anthu omvela adzakhala na thanzi labwino na moyo wosatha. Baibo imakamba kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.

Ŵelengani Yobu 14:14, 15; Luka 7:11-17; na Macitidwe 24:15.

Ningazipemphela Bwanji Kuti Mulungu Azinimvela?

Mwamuna apemphela

CIMENE ANTHU AMAFUNSILA FUNSO IMENEYI: Anthu mu machechi onse amapemphela. Koma ambili amaona kuti mapemphelo awo sayankhidwa.

ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA: Yesu anatiphunzitsa kuti sitiyenela kupeleka mapemphelo amene anthu ena anakonzelatu. Iye anakamba kuti: “Popemphela musabwelezebweleze cabe iyai.” (Mateyu 6:7) Ngati tifuna kuti Mulungu azimvela mapemphelo athu, tifunika kupemphela mmene iye amafunila. Kuti ticite zimenezi, tifunikila kudziŵa cifunilo ca Mulungu na kupemphela mmene iye amafunila. Pa 1 Yohane 5:14 pamakamba kuti: “Ngati tipempha kanthu monga mwa cifunilo [ca Mulungu], atimvela.”

Ŵelengani Salmo 65:2; Yohane 14:6,14; na 1 Yohane 3:22.

Ningapeze Bwanji Cimwemwe mu Moyo Wanga?

Mzimai afuna-funa cimwemwe mwa kuŵelenga Baibo

CIMENE ANTHU AMAFUNSILA FUNSO IMENEYI: Anthu ambili amaganiza kuti kukhala olemela, kudziŵika kapena kuoneka okongola ndiye kumabweletsa cimwemwe. Conco, iwo amalimbikila kupeza zinthu zimenezi, koma ngakhale azipeze, cimwemwe samacipeza.

ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA: Yesu anasonyeza cinsinsi copezela cimwemwe pamene anakamba kuti: ‘Osangalala ali iwo amene amazindikila zosoŵa zawo zauzimu.” (Mateyu 5:3, NW) Pali njila imodzi cabe imene tingapezele cimwemwe cazoona. Tiyenela kucitapo kanthu kuti tiphunzile na kudziŵa coonadi ponena za Mulungu, na vimene iye amafuna kuticitila. Coonadi cimeneco cimapezeka mu Baibo. Tikaphunzila zimenezo, tidzadziŵa vinthu vofunika kwambili pamoyo na vosafunika kwenikweni. Ngati tilola kuti Baibo izititsogolela pa zosankha na zocita zathu, moyo wathu udzakhala watanthauzo kwambili.—Luka 11:28.

Ŵelengani Miyambo 3:5, 6, 13-18 na 1 Timoteo 6:9, 10.

Apa takambako pang’ono cabe za mayankho a mu Baibo pa mafunso 6 aja. Kodi mufuna kudziŵa zambili? Ngati na imwe muli na njala yauzimu, mudzafuna kudziŵa zambili. Kapena mumadzifunsanso mafunso ena monga aya: ‘Ngati Mulungu amatisamalila, ni cifukwa ciyani amalola kuti anthu azikumana na voipa na mavuto? Nanga ine ningacite ciyani kuti banja yanga ikhale yacimwemwe?’ Baibo imapeleka mayankho omveka bwino pa mafunso aya na ena ambili.

Koma masiku ano anthu ambili safuna kupeza mayankho mu Baibo. Amaona Baibo kuti ni buku ikulu kwambili ndipo yovuta kuimvetsetsa. Kodi mungafune kuti munthu wina akuthandizeni kupeza mayankho mu Baibo? A Mboni za Yehova amapeleka vinthu viŵili vimene vingakuthandizeni.

Cinthu coyamba ni buku yakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Buku imeneyi imathandiza anthu kupeza mayankho omveka a mu Baibo pa mafunso ofunika, ngakhale kwa anthu amene sapeza nthawi yokwanila. Caciŵili ni pulogilamu yamahala yophunzila Baibo. Wa Mboni za Yehova amene amakhala pafupi na imwe, amenenso amadziŵa kuphunzitsa Baibo, angazibwela kunyumba kwanu kapena kumalo amene mungafune. Iye angaziphunzila Baibo na imwe kwa nthawi ing’ono cabe wiki iliyonse. Pulogilamu imeneyi yathandiza anthu mamiliyoni padziko lonse. Ambili afika pokamba kuti: “Izi ndiye zoona!”

Palibe cuma cimene tingapeze coposa cimeneci. Coonadi ca mu Baibo cimatimasula ku vinthu vamizimu, ku viphunzitso vosokoneza na ku mantha osiyanasiyana. Coonadi cimatipatsa ciyembekezo, moyo watanthauzo na cimwemwe. Yesu anakamba kuti: “Mudzazindikila coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.”—Yohane 8:32.

1. Mwamuna aphunzila zimene Baibo imaphunzitsa; 2. Mzimai aphunzila zimene Baibo imaphunzitsa