Onani zimene zilipo

Kodi Ndani Maka-Maka Amene Akulamulila Dzikoli?

Kodi Ndani Maka-Maka Amene Akulamulila Dzikoli?

Kodi muganiza kuti ndi . . .

  • Mulungu?

  • anthu?

  • wina wake?

 ZIMENE BAIBO IMANENA

“Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.

“Mwana wa Mulungu anabwela . . . kuti aononge nchito za Mdyelekezi.”—1 John 3:8, New Century Version.

UBWINO WOKHULUPILILA ZIMENEZI

Mudzamvetsetsa cifukwa cake padziko pali mavuto.—Chivumbulutso 12:12.

Mudzakhala ndi ciyembekezo cakuti zinthu padziko zidzakhala bwino mtsogolo.—1 Yohane 2:17.

 KODI TINGAKHULUPILILEDI ZIMENE BAIBO IMANENA?

Inde, pa zifukwa zitatu izi:

  • Ulamulilo wa Satana udzaonongedwa. Yehova ndi wokonzeka kwambili kucotsa ulamulilo wa Satana padziko lapansi. Iye walonjeza kuti ‘adzaononga Mdyelekezi’ ndi kukonzanso zinthu zonse zimene Satana waononga.—Aheberi 2:14, Baibulo la Dziko Latsopano.

  • Mulungu wasankha Yesu Kristu kukhala wolamulila wa dziko. Yesu ndi wosiyana kwambili ndi wolamulila wa dzikoli amene ndi wankhanza ndi wodzikonda. Ponena za ulamulilo wa Yesu, Mulungu walonjeza kuti: “Adzamvela cisoni munthu wonyozeka ndi wosauka . . . Adzaombola miyoyo yao ku cipsinjo ndi ciwawa.”—Salimo 72:13, 14.

  • Mulungu sanama. Baibo imakamba mosapita m’mbali kuti: “N’zosatheka kuti Mulungu aname.” (Aheberi 6:18) Yehova akalonjeza zinthu, zimakhala monga kuti zacitika kale. (Yesaya 55:10, 11) ‘Wolamulila wa dzikoli adzaponyedwa kunja.’—Yohane 12:31.

Ngati mulibe Baibo, mungaiŵelengele pa Intaneti pa adiresi iyi: www.jw.org/nya (Pitani pa MABUKU > BAIBO)

 GANIZILANI FUNSO ILI

Kodi dzikoli lidzakhala bwanji wolamulila wake akacotsedwapo?

Baibo imayankha funso limeneli pa SALIMO 37:10, 11 ndi pa CHIVUMBULUTSO 21:3, 4.