Kodi mungayankhe kuti . . .

  • inde?

  • iyai?

  • kapena?

 ZIMENE BAIBO IMANENA

“Kudzakhala kuuka.”—Machitidwe 24:15, Baibulo la Dziko Latsopano.

MAPINDU OKHULUPILILA KUTI AKUFA ADZAUKA

Kukhulupilila zimenezi kudzakutonthozani munthu amene mumakonda akamwalila.—2 Akorinto 1:3, 4.

Simudzaopa imfa mopambanitsa.—Aheberi 2:15.

Mudzakhala ndi ciyembekezo ceni-ceni cakuti mudzaonanso okondedwa anu amene anamwalila.—Yohane 5:28, 29.

 KODI TINGAKHULUPILILEDI ZIMENE BAIBO IMANENA?

Inde, pa zifukwa zitatu izi:

  • Mulungu ndiye Mlengi wa moyo. Baibo imacha Yehova Mulungu kuti ndi “kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9; Machitidwe 17:24, 25) Iye amene anapatsa moyo colengedwa ciliconse, sangalephele kubwezeletsa moyo wa munthu amene wamwalila.

  • Mulungu anaukitsapo anthu m’nthawi zakale. Baibo imafotokoza za anthu 8 amene anaukitsidwa padziko lapansi. Anthu amenewo anali ana, akulu, amuna ndi akazi. Ena anali akufa kwa nthawi yocepa, koma mmodzi anali m’manda kwa masiku anai.—Yohane 11:39-44.

  • Mulungu ndi wofunitsitsa kuukitsanso akufa. Yehova amadana ndi imfa, ndipo amaiona kuti ndi mdani. (1 Akorinto 15:26) Iye ‘amalaka-laka’ kugonjetsa mdani ameneyo. Iye adzacotsapo imfa mwa kuukitsa akufa. Mulungu amafunitsitsa kuukitsa anthu amene ali m’cikumbukilo cake kuti adzakhalenso ndi moyo padziko lapansi.—Yobu 14:14, 15.

 GANIZILANI FUNSO ILI

N’cifukwa ciani timakalamba ndi kufa?

Baibo imayankha funso limenelo pa GENESIS 3:17-19 ndi pa AROMA 5:12.