NYIMBO ZOPEKEDWA KOYAMBA

Mphindi Iliyonse

Cinyanja
Mphindi Iliyonse
https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/502900115/univ/art/502900115_univ_sqr_xl.jpg

Mphindi Iliyonse

Mphindi Iliyonse

Citani daunilodi:

  1. 1. Moyo wathu uli ngati mame

    Amene samakhalitsa.

    Tiyeni tisonyeze cikondi

    Kwa ena pamene tili ndi nthawi.

    (KOLASI)

    Ngati ndingazengeleze, ndingataye nthawi

    Yofunika kuonetsa cikondi

    Okondedwa anga onse. Sin’dziwa za mawa

    Sindifuna kukadziimba mlandu.

    Ndidzagwilitsila nchito bwino mphindi iliyonse.

  2. 2. Poona cikondi komanso

    Kukongola kwa cilengedwe

    Ca M’lungu, zimandilimbikitsa

    Kuti ndizimutumikila mwakhama.

    (KOLASI)

    Ngati ndingazengeleze, ndingataye nthawi

    Yofunika kuonetsa cikondi

    Okondedwa anga onse. Sin’dziwa za mawa

    Sindifuna kukadziimba mlandu.

    Ndidzagwilitsila nchito bwino mphindi iliyonse.

    (BILIJI)

    M’tsogolo M’lungu adzatipatsa

    Dziko labwino zedi.

    Pamene tikuyembekezela

    Tim’patse nthawi yathu.

    (KOLASI)

    Ngati ndingazengeleze, ndingataye nthawi

    Yofunika kuonetsa cikondi

    Okondedwa anga onse. Sindidziwa za mawa

    Sindifuna kukadziimba mlandu.

    Conco ndidzagwilitsa nchito bwino mphindi iliyonse.