Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

WATCHTOWER LIBRARY

Ikani Watchtower Library

Ikani Watchtower Library

Mungathe kuipanga dawunilodi ndipo kukula kwake ndi 2 GB. Ngati simungathe kupanga dawunilodi chifukwa cha vuto la intaneti kapena la ndalama, mukhoza kukatenga DVD yoikira pulogalamuyi ku mpingo wa Mboni za Yehova m’dera lanu. Dinani batani lakuti Pangani Dawunilodi kuti mudziwe ngati Watchtower Library ikupezeka m’chiyankhulo chanu.

 

Zimene Kompyuta Yanu Iyenera Kukhala Nazo Kuti Muthe Kugwiritsa Ntchito Laibulaleyi

Kuti muthe kugwiritsa ntchito Watchtower Library, kompyuta kapena laputopu yanu ikhale yogwirizana ndi processor ya Pentium kapena ina yamphamvu kuposa imeneyi. Ikhale yoti muli Microsoft Windows 7 kapena kuposa ndipo RAM yake ikhale yosachepera 48 MB komanso hard drive ya kompyutayo ikhale yoyambira 3 GB ku C: drive.

Dziwani izi: Ngati kompyuta yanu ili ndi Microsoft Windows 7, choyamba muyenera kupanga kaye dawunilodi ndi kuikamo pulogalamu ya pakompyuta yothandiza kuti kompyutayo ikwanitse kutsegula failo ya ISO. Mungathe kupeza pulogalamuyi pa webusaiti ya Microsoft.

 

Malangizo Okuthandizani Kuika Laibulaleyi mu Kompyuta

Tsatirani malangizo ali m’munsimu kuti mupange dawunilodi ndi kuika Watchtower Library:

  • 1. Dinani batani lakuti Pangani Dawunilodi lomwe lili patsamba lino.

  • 2. Sankhani chinenero podina pakabokosi komwe kali ndi muvi woloza pansi kenako dinani batani lopangira Dawunilodi.

  • 3. Dinani kumanja kwa mausi pa failo ya ISO yomwe mwapanga dawunilodi, kenako dinani mawu akuti Mount. (Dziwani izi: Ngati mukugwiritsa ntchito pulogalamu ina ya pakompyuta yothandiza kutsegula failo ya ISO malangizo ake angasiyane. Choncho muyenera kutsatira malangizo omwe mwauzidwa pa pulogalamu inayo.)

  • 4. Dinani kawiri failo ya WTLSetup.exe, kenako tsatirani malangizo omwe akuonekawo kuti muike Watchtower Library.