Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

JW LAIBULALE

Ikani Kachizindikiro Kokuthandizani Kukumbukira pa Zipangizo za Android

Ikani Kachizindikiro Kokuthandizani Kukumbukira pa Zipangizo za Android

JW Laibulale imakulolani kuika chizindikiro pa chinthu chilichonse chomwe mukuwerenga, mofanana ndi mmene mumaikira kachingwe kapena chizindikiro chilichonse m’buku lenileni kuti mudzakumbukire pamene munalekezera kuwerenga. Buku lililonse lomwe lili mu JW Laibulale limakhala ndi zizindikiro zokwana 10 zokuthandizani kukumbukira pamene munalekeza.

Kuti mugwiritse ntchito zizindikirozi, tsatirani malangizo awa:

 Kuika Chizindikiro Chatsopano

Mukhoza kuika chizindikiro pankhani kapena mutu umene mwalekeza komanso mukhoza kuika chizindikiro pandime kapena vesi limene mwalekeza pamene mukuwerenga.

Kuti muike chizindikiro pankhani kapena mutu wonse, dinani kachizindikiro kamene kali kumanja kwa kachizindikiro kooneka ngati galasi. Mukatero, zizindikiro za mitundu yosiyanasiyana zimabwera. Kenako sankhani chizindikiro chimene chilibe mawu ena alionse.

Kuti muike chizindikiro pandime kapena pavesi la m’Baibulo, dinani pavesi kapena ndimeyo ndipo pamabwera kabokosi kokhala ndi chizindikiro chija. Dinani chizindikirocho ndipo kenako sankhani chizindikiro chomwe mukufuna.

 Kupita Pamene Munaika Chizindikiro

Kuti mupite pamene pali chizindikiro, tsegulani buku limene lili ndi chizindikirocho, kenako dinani chizindikiro cham’mwamba chija. Mukatero dinani pa chizindikiro chimene mukufuna.

 Kusintha Chizindikiro

Mukaika chizindikiro, mukhoza kuchifufuta kapena kuchisintha kuti chikhale pamalo ena.

Kuti mufufute chizindikiro, dinani pachizindikirocho, kenako dinani pamene pali timadontho titatu pafupi ndi chizindikiro chimene mukufuna kufufuta. Kenako dinani pamene palembedwa kuti Delete.

Kuti musinthe malo omwe pali chizindikiro n’kuchiika pamene mwalekeza lero, dinani pamene mwalekezapo. Kenako dinani pachizindikiro chimene chabwera. Mukatero, dinani patimadontho titatu tomwe tili pafupi ndi chizindikiro chimene munaika chija, kenako dinani pamene palembedwa kuti Replace. Mukatero chizindikirocho chipita pamene mwalekeza panopa. Zimenezi n’zothandiza kuti muzidziwa pamene mwalekeza mukamawerenga. Mwachitsanzo, mukhoza kudziwa pamene mwalekeza powerenga Baibulo tsiku ndi tsiku.

Zimenezi zinayamba kutheka kuyambira mu JW Laibulale 1.2 yomwe inatuluka mu May 2014. Laibulaleyi imagwirizana ndi zipangizo zomwe zimagwiritsa ntchito pulogalamu ya Android 2.3 kapena iliyonse yomwe inatuluka pambuyo pake. Ngati zizindikirozi sizikuoneka, tsatirani malangizo omwe ali m’nkhani yakuti, “Yambani Kugwiritsa Ntchito JW Laibulale ya pa Zipangizo za Android” pansi pa mutu wakuti Kupeza Zinthu Zatsopano.