Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

JW LAIBULALE

Yambani Kugwiritsa Ntchito JW Laibulale ya pa Zipangizo za Android

Yambani Kugwiritsa Ntchito JW Laibulale ya pa Zipangizo za Android

Zikomo kwambiri chifukwa chosankha kugwiritsa ntchito JW Laibulale. Pulogalamuyi inakonzedwa kuti izithandiza anthu kuwerenga ndiponso kuphunzira Baibulo. Pali bokosi limene lili ndi zinthu zikuluzikulu za mu pulogalamuyi. Kuti mutsegule bokosili, yendetsani chala chanu pasikirini kuchokera kumanzere kupita kumanja kapena pitani pabatani la Menyu lomwe lili kumanzere m’mwamba.

 Baibulo

Mukadina pamene palembedwa kuti Bible, mupeza Mabaibulo a zinenero zosiyanasiyana. Kuti mutsegule Baibulo, dinani buku la m’Baibulo limene mukufuna kenako pitani pa chaputala chimene mukufuna kuwerenga. Mukamawerenga mungathenso kuona mawu am’munsi, malifalensi olozera ku mavesi ena ndiponso mmene vesilo linamasulidwira m’Mabaibulo ena.

Kuti muwerenge lemba lina, tsegulaninso bokosi lija kenako dinaninso pamene palembedwa kuti Bible kuti muone mabuku onse a m’Baibulo.

 Mabuku ndi Zinthu Zina

Mukadina pamene palembedwa kuti Publications mupeza mabuku, timapepala, timabuku, mavidiyo komanso zinthu zongomvetsera za zinenero zosiyanasiyana. Kuti muwerenge nkhani inayake, sankhani buku, kenako nkhani imene mukufuna. Mukamawerenga mukhozanso kutsegula malemba amene ali m’nkhaniyo. Ngati mutadina pavesi limene mwatsegulalo, mukhoza kutsegula chaputala chonse chimene pachokera lembalo.

Kuti mutsegule buku lina, bwereraninso poyambirira paja, kenako tsegulaninso pamene alemba kuti Publications kuti muone mayina a mabuku onse.

 Lemba la Tsiku

Kuti mutsegule lemba la tsiku, tsegulaninso bokosi lija n’kusankha mawu akuti Daily Text.

 Intaneti

Mbali imene alemba kuti Online m’bokosi lija imakuthandizani kutsegula mawebusaiti athu ovomerezeka.

 Kupeza Zinthu Zatsopano

Onetsetsani kuti JW Laibulale yanu mukumaichita “update” pafupipafupi kuti muzitha kugwiritsa ntchito zinthu zatsopano zimene zaikidwa.

Mungachite bwino kuonetsetsa kuti muli ndi pulogalamu yatsopano ya Android yogwirizana ndi chipangizo chanucho. Kuti mudziwe zambiri dinani linki iyi: https://support.google.com/nexus/answer/4457705.

Ngati mukufuna, mukhoza kutchera chipangizo chanucho kuti chizichita chokha “update” mapulogalamu omwe ali m’chipangizocho. Kuti mudziwe zambiri dinani linki iyi: https://support.google.com/googleplay/answer/113412.