Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

JW LAIBULALE

Onani Zimene Munatsegula pa Zipangizo za Android

Onani Zimene Munatsegula pa Zipangizo za Android

JW Laibulale imasunga nkhani komanso machaputala a m’Baibulo amene munawerenga. Zimenezi ndi zothandiza mukafuna kutsegulanso lemba limene munawerenga kale.

Kuti zimenezi zitheke, chitani zotsatirazi:

 Kuona Zimene Munatsegula

Dinani pa batani la History (looneka ngati wotchi ya mivi) kuti muone malemba komanso nkhani zomwe mwawerenga posachedwapa. Dinani lemba kapena nkhani imene munatsegulayo ndipo itsegukanso.

 Kuchotsa Zimene Munatsegula

Dinani batani la History kuti muone malemba komanso nkhani zomwe mwawerenga posachedwapa. Kenako dinani pamene palembedwa kuti Clear.

Zimenezi zinayamba kutheka kuyambira mu JW Laibulale 1.2 yomwe inatuluka mu May 2014. Laibulaleyi imagwirizana ndi zipangizo zomwe zimagwiritsa ntchito pulogalamu ya Android 2.3 kapena iliyonse yomwe inatuluka pambuyo pake. Ngati batani lochitira zimenezi silikuoneka, tsatirani malangizo omwe ali m’nkhani yakuti, “Yambani Kugwiritsa Ntchito JW Laibulale ya pa Zipangizo za Android” pansi pa mutu wakuti Kupeza Zinthu Zatsopano.