Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

JW LAIBULALE

Mukhoza Kusintha Zina ndi Zina Mukamawerenga pa Zipangizo za Android

Mukhoza Kusintha Zina ndi Zina Mukamawerenga pa Zipangizo za Android

Pali zinthu zingapo zimene zinaikidwa mu JW Laibulale zomwe zingakuthandizeni mukamawerenga zinthu. Zinthu zimenezi zikupezeka pamwamba pa sikirini mukamawerenga Baibulo kapena nkhani inayake.

Mukhoza kudina pakabatani kokhala ngati timadontho titatu kuti muone zinthu zinanso zomwe mungakonde kusintha.

Chitani zotsatirazi kuti musinthe zinthu zimene mukufuna:

 Kusintha Chinenero

Mukhoza kusintha chinenero kuti muwerenge nkhani kapena chaputala cha m’Baibulo m’chinenero china.

  • Kuti muchite zimenezi, dinani pamene palembedwa kuti Languages kuti muone zinenero zonse zomwe zili ndi nkhani kapena chaputala chomwe mukuwerengacho. Zinenero zomwe mumakonda kugwiritsa ntchito zimapezeka kumayambiriro kwa zinenero zinazo. Mukhozanso kulemba chinenero chimene mukufunacho ndipo ngati chilipo chimabwera.

  • Zinenero zomwe simunapange dawunilodi zimakhala ndi kachizindikiro ka mtambo. Ngati mukufuna kupanga dawunilodi chinthu cha m’chinenero chinachake, ingodinani pa chinenerocho. Chikamaliza kupanga dawunilodi, kachizindikiro ka mtambo kaja kamachoka. Ngati mukufuna kuwerenga nkhaniyo ingodinaninso chinenerocho ndipo itseguka.

 Kukulitsa Kapena Kuchepetsa Mawu

Mukhoza kusintha zilembo kuti zikule kapena zichepe mmene mukufunira.

Kuti muchite zimenezi, dinani pamene palembedwa kuti Text Settings ndipo pamabwera kabokosi komwe kamakhala ndi kadontho. Dinani kadonthoko n’kukayendetsa kupita kumanja kapena kumanzere. Mukamapititsa kumanja, zilembo zimakula pomwe mukapititsa kumanzere, zimachepa. Mukangosintha, ndiye kuti zilembo zizioneka choncho mukatsegula buku kapena nkhani iliyonse.

 Kusankha Mmene Nkhaniyo Itaonekere

Nkhani zina zikhoza kuoneka mmene zilili m’buku kapena ndi mawu okha. Dinani batani loyenera kuti muwerenge nkhaniyo mmene ilili m’buku kapena ngati mawu basi.

  • Ioneke Mmene Ilili M’buku: Mukasankha kaonekedwe kameneka mumaona nkhaniyo mmene ikuonekera m’buku lenileni. Ena amakonda kuti zizioneka chonchi akamaimba nyimbo chifukwa amatha kuona manotsi a nyimboyo.

  • Ioneke Ngati Mawu Basi: Mukasankha kaonekedwe kameneka zimakhala zotheka kutsegula mavesi amene ali mu nkhaniyo ndipo kakulidwe ka mawu ake kamafanana ndi kamene munasankha pa nkhani zina zonse.

 Kutsegula mu Pulogalamu Ina

Mukadina pamene alemba kuti Open in . . . mumatha kuona mabuku omwe ali mu JW Laibulale pogwiritsa ntchito mapulogalamu ena.

Mukadina pamenepa mumatha kuona mapulogalamu amene alipo omwe angatsegule zimene mukuwerengazo. Mwachitsanzo, mungasankhe kuti mutsegule Laibulale ya pa Intaneti kuti muone nkhaniyo mu LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower.

 Kusankha Baibulo Lomwe Mukufuna

Mukadina mavesi omwe ali munkhani imene mukuwerenga, mavesiwo amaoneka. Ndiye mukapita m’munsi mwa mavesiwo mumapeza mawu akuti Customize. Mukadina pamenepa pamabwera kabokosi ndipo mukhoza kusankha Mabaibulo omwe mukufuna kuti azioneka mukatsegula lemba.

Dinani kabatani komwe kali ndi chizindikiro cha + kuti muwonjezere Baibulo kapena dinani chizindikiro cha ngati mukufuna kuchotsa Baibulolo. Dinani pamene pali timizere titatu osasiya ndipo kenako yendetsani chalacho kupita m’mwamba ngati mukufuna kuti lipite m’mwamba, kapena pititsani m’munsi ngati mukufuna kuti likhale m’munsi mwa mabaibulo ena.

Onani nkhani yakuti, “Pangani Dawunilodi Mabaibulo pa Zipangizo za Android” kuti mudziwe mmene mungapangire dawunilodi Mabaibulo ena mu JW Laibulale.

Zimenezi zinayamba kutheka kuyambira mu JW Laibulale 1.4 yomwe inatuluka mu February 2015. Laibulaleyi imagwirizana ndi zipangizo zomwe zimagwiritsa ntchito pulogalamu ya Android 2.3 kapena iliyonse yomwe inatuluka pambuyo pake. Ngati mwayesa kuchita zimenezi koma sizikutheka, tsatirani malangizo omwe ali m’nkhani yakuti, “Yambani Kugwiritsa Ntchito JW Laibulale pa Zipangizo za Android” pansi pa mutu wakuti Kupeza Zinthu Zatsopano.