Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

JW LAIBULALE

Pangani Dawunilodi ndi Kusunga Mabuku pa Zipangizo za Android

Pangani Dawunilodi ndi Kusunga Mabuku pa Zipangizo za Android

Pali mabuku, timabuku, timapepala komanso mavidiyo ambirimbiri omwe mungawerenge komanso kuonera pa JW Laibulale popanda kulowa pa intaneti.

Tsatirani malangizo ali m’munsiwa kuti mupange dawunilodi komanso kusunga zinthu zimenezi:

 Kupanga Dawunilodi

Mukhoza kupanga dawunilodi mabuku komanso zinthu zina mmene mukufunira kuti muziwerenga komanso kuphunzira popanda kulowa pa intaneti.

  • Dinani pamene palembedwa kuti Publications kuti muone zinthu zimene zilipo.

  • Dinani pamene palembedwa kuti Languages kuti muone zinenero zonse zimene zinthu zake zikupezeka mulaibulaleyi. Kenako sankhani chinenero chimene mukufuna. Zinenero zimene mumakonda kugwiritsa ntchito zimakhala pamwamba pa zinenero zina. Mukhozanso kusankha chinenero chinachake chimene mukufuna polemba dzina la chinenerocho.

Pali njira zingapo zomwe mungapezere mabuku komanso zinthu zina mu JW Laibulale.

Dinani pamene palembedwa kuti By Type kuti muone mabuku komanso zinthu zina zonse zimene zili m’chinenerocho zogawidwa m’magulu mogwirizana ndi mtundu wake monga mabuku, timapepala kapena mavidiyo. Mukadina mitundu ina, mumafunikanso kusankha zinthu zina. Mwachitsanzo, mukafuna Nsanja ya Olonda mumafunika kusankhanso chaka chimene inatuluka, pomwe mukafuna mavidiyo mumafunika kusankhanso gulu la mavidiyowo. Dinani batani lakuti All Types kuti mubwererenso pamwamba.

Pamene palembedwa kuti What’s New pamapezeka mabuku komanso zinthu zina zomwe zangotulutsidwa kumene m’chinenero chimene mwasankhacho.

Buku kapena zinthu zina zomwe simunapange dawunilodi zimakhala ndi kachizindikiro ka mtambo. Ngati mukufuna kupanga dawunilodi ingodinani buku kapena chinthu chimene mukufunacho. Chinthucho chikamaliza kupanga dawunilodi, kachizindikiro kaja kamachoka. Kuti muwerenge kapena kuonera chinthucho, ingochidinaninso.

Pamene palembedwa kuti Downloaded pamapezeka zinthu zonse zimene munapanga dawunilodi. Mukhoza kusankha kuti zinthuzo zisanjidwe m’magulu a zimene mumatsegulatsegula (Frequently Used), zimene simutsegulatsegula (Rarely Used) kapena zinthu zikuluzikulu (Largest Size).

Kufufuta Chinthu

 Mukhoza kufufuta buku kapena chinthu china chimene simukuchifunanso. Mungachitenso zimenezi ngati mukufuna kupeza malo oti muike zinthu zina.

Dinani pamene palembedwa kuti Publications. Kenako dinani gulu la zinthu zimene mukufunazo (mwachitsanzo Books) kuti muone zinthu zonse zimene zili pamenepo. Pamene pali buku kapena chinthu chimene mukufuna kufufutacho, dinani kabatani kokhala ngati timadontho titatu, kenako dinani mawu akuti Delete.

Ngati mukufuna kupeza malo oika zinthu zina, mukhoza kuchotsa zinthu zimene simugwiritsa ntchito kawirikawiri kapena zinthu zikuluzikulu. Dinani pamene palembedwa kuti Publications. Kenako pitani pamene palembedwa kuti Downloaded ndipo musankhe zimene mukufuna. Mukhoza kudina Rarely Used kapena Largest Size, kenako n’kufufuta zinthu zomwe simukuzifunazo.

Kudziwa Pamene Zinthu Zasinthidwa

 Nthawi zina mabuku komanso zinthu zina zimakonzedwanso moti mungafunike kupanganso dawunilodi zinthuzo.

Buku kapena zinthu zomwe zakonzedwanso zimakhala ndi kachizindikiro kokhala ngati timivi tiwiri tozungulira. Mukadina chinthucho, pamabwera uthenga wosonyeza kuti chinthucho chakonzedwanso. Dinani batani lakuti Download kuti mupeze chinthu chomwe chakonzedwansocho kapena dinani batani lakuti Later kuti mubagwiritsa ntchito kaye chinthu chimene muli nacho kale m’chipangizo chanu.

Kuti mudziwe ngati buku kapena chinthu chimene muli nacho chasinthidwa, dinani pamene palembedwa kuti Publications. Ngati pali buku kapena chinthu chimene chasinthidwa, pamakhala kabatani kokhala ndi mawu akuti Pending Updates. Dinani batanilo kuti muone zinthu zomwe zilipo. Dinani chinthu chimene mukufunacho kapena dinani batani lakuti Update All kuti mupange dawunilodi zonsezo.

Zimenezi zinayamba kutheka kuyambira mu JW Laibulale 1.4 yomwe inatuluka mu February 2015. Laibulaleyi imagwirizana ndi zipangizo zomwe zimagwiritsa ntchito pulogalamu ya Android 2.3 kapena iliyonse yomwe inatuluka pambuyo pake. Ngati mwayesa kuchita zimenezi koma sizikutheka, tsatirani malangizo omwe ali m’nkhani yakuti, “Yambani Kugwiritsa Ntchito JW Laibulale ya pa Zipangizo za Android” pansi pa mutu wakuti Kupeza Zinthu Zatsopano.