Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

JW LAIBULALE

Pangani Dawunilodi ndi Kusunga Mabaibulo pa Zipangizo za Android

Pangani Dawunilodi ndi Kusunga Mabaibulo pa Zipangizo za Android

JW Laibulale inakonzedwa kuti munthu azigwiritsa ntchito powerenga komanso kuphunzira Baibulo.

Tsatirani malangizo ali m’munsiwa kuti mupange dawunilodi komanso kusunga Mabaibulo:

 Kupanga Dawunilodi Baibulo

Mukhoza kupanga dawunilodi Mabaibulo a zinenero zosiyanasiyana oti muzigwiritsa ntchito powerenga komanso kuphunzira mukakhala kuti simuli pa intaneti.

  • Dinani pamene palembedwa kuti Bible kuti muone mabuku onse a m’Baibulo.

  • Dinani pamene palembedwa kuti Languages kuti muone Mabaibulo onse amene alipo. Mabaibulo azinenero zomwe mumakonda kugwiritsa ntchito amakhala kumayambiriro kwa Mabaibulo ena. Mukhozanso kufufuza polemba chinenero chimene mukufuna kapena dzina la Baibulo limene mukufunalo. Mwachitsanzo, mungalembe “int” kuti mupeze Baibulo la Kingdom Interlinear lomwe lili m’Chingelezi kapena mungalembe mawu akuti “port” kuti mupeze Mabaibulo onse a Chipwitikizi.

  • Baibulo lomwe simunapange dawunilodi limakhala ndi kachizindikiro ka mtambo. Ngati mukufuna kupanga dawunilodi, ingodinani Baibulolo. Baibulolo likamaliza kupanga dawunilodi, kachizindikiro kaja kamachoka. Mukafuna kuwerenga, ingodinaninso Baibulolo.

Ngati simukupeza Baibulo limene mukufuna, mungayesenso nthawi ina. Mabaibulo a zinenero zina amaikidwa pa intaneti akangomalizidwa kukonzedwa.

 Kufufuta Baibulo

Mukhoza kufufuta Baibulo limene simukulifunanso. Mungachitenso zimenezi ngati mukufuna kupeza malo oti muike zinthu zina.

Dinani pamene palembedwa kuti Bible. Kenako dinaninso pamene palembedwa kuti Languages kuti muone Mabaibulo onse. Dinani pamene pali timadontho titatu kumanja kwa Baibulo mukufunalo, kenako dinani pamene alemba kuti Delete.

 Kudziwa Pamene Baibulo Lasinthidwa

Nthawi zina, Mabaibulo amakonzedwanso moti mungafunike kupanganso dawunilodi Baibulo loti linalimo kale.

Baibulo lomwe lakonzedwanso limakhala ndi kachizindikiro kokhala ngati timivi tiwiri tozungulira. Mukadina Baibulolo, pamabwera uthenga wosonyeza kuti lakonzedwanso. Dinani batani lakuti Download kuti mupeze Baibulo latsopanolo kapena dinani batani lakuti Later kuti mubagwiritsa ntchito kaye Baibulo lomwe lili kale m’chipangizo chanu.

Zimenezi zinayamba kutheka kuyambira mu JW Laibulale 1.4 yomwe inatuluka mu February 2015. Laibulaleyi imagwirizana ndi zipangizo zomwe zimagwiritsa ntchito pulogalamu ya Android 2.3 kapena iliyonse yomwe inatuluka pambuyo pake. Ngati mwayesa kuchita zimenezi koma sizikutheka, tsatirani malangizo omwe ali m’nkhani yakuti, “Yambani Kugwiritsa Ntchito JW Laibulale ya pa Zipangizo za Android” pansi pa mutu wakuti Kupeza Zinthu Zatsopano.