Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

JW LAIBULALE

Mukhoza Kuchekenira Mfundo Zofunika pa Zipangizo za Android

Mukhoza Kuchekenira Mfundo Zofunika pa Zipangizo za Android

Mukamawerenga nkhani mu JW Laibulale, mukhoza kuchekenira mawu komanso ziganizo zomwe mukufuna.

Chitani zotsatirazi ngati mukufuna kuchekenira mawu kapena chiganizo:

 Kuchekenira

Pali njira ziwiri zomwe mungachekenire mawu.

Dinani kwa kanthawi mawu amodzi ndipo amasintha mtundu komanso pamabwera tizizindikiro tiwiri m’mbali mwake. Mungasunthe tizizindikiroti mpaka pamene mukufuna kulekezera kuchekenirako. Pamwamba pa mawu amene mukufuna kuchekenirawo pamabwera kabokosi komwe kamakhala ndi madontho a mitundu yosiyanasiyana, kenako dinani pa mtundu umene mukufuna ndipo mawuwo achekeniridwa ndi mtundu umene mwasankhawo.

Kuti muchekenire mawu kamodzin’kamodzi, dinani pamawu mukufunawo kwa kanthawi ndipo kenako yendetsani chala chanu mpaka pamene mukufuna kulekeza. Mukangosiya, mawuwo amachekeniridwa ndipo pamwamba pake pamabwera kabokosi kaja ndipo kamachoka pakangodutsa kanthawi pang’ono. Mukhoza kugwiritsa ntchito kabokosi kameneka posintha mtundu kapena kufufuta chekeni chimene munagwiritsa ntchito.

 Kusintha Mtundu

Kuti musinthe mtundu, dinani mawu amene munachekenirawo ndipo kabokosi kaja kamabweranso. Zikatero dinani mtundu umene mukufuna, ndipo mawuwo achekeniridwa ndi mtunduwo. Kuti mufufute chekeni, dinani kachizindikiro ka bini komwe kali m’kabokosiko.

Zimenezi zinayamba kutheka kuyambira mu JW Laibulale 1.6 yomwe inatuluka mu November 2015. Laibulaleyi imagwirizana ndi zipangizo zomwe zimagwiritsa ntchito pulogalamu ya Android 4.0 kapena iliyonse yomwe inatuluka pambuyo pake. Ngati mwayesa kuchita zimenezi koma sizikutheka, tsatirani malangizo omwe ali m’nkhani yakuti, “Yambani Kugwiritsa Ntchito JW Laibulale ya pa Zipangizo za Android” pansi pa mutu wakuti Pezani Zinthu Zatsopano.