Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

JW LIBRARY

Ikani JW Library M’chipangizo cha Android Ngati Simungathe Kupanga Dawunilodi Kudzera pa App Store

Ikani JW Library M’chipangizo cha Android Ngati Simungathe Kupanga Dawunilodi Kudzera pa App Store

Ngati simungathe kuika JW Library m’chipangizo chanu cha Android kudzera pa app store yovomerezeka monga pa Google Play Store kapena pa Amazon Appstore, mukhoza kuika laibulaleyi pogwiritsa ntchito JW Library Android Package Kit (APK).

Kuti muike JW Library APK m’chipangizo chanu, pitani ku ma settings ndipo dinani mawu akuti “install unknown apps” kapena “allow installation from unknown sources.” Onani malangizo omwe ali mu chipangizo chanu cha Android kuti mudziwe mmene mungachitire zimenezi.

Tsatirani malangizo ali m’munsimu kuti mupange dawunilodi komanso kuika JW Library APK:

  1. Dinani batani lakuti Pangani Dawunilodi lomwe lili patsamba lino kuti musunge failo ya APK m’chipangizo chanu.

  2. Pezani failo ya APK m’chipangizo chanu, kenako dinani failoyo kuti muike JW Library.

Pambuyo poti mwaika JW Library APK, muziona pafupipafupi ngati paikidwa JW Library APK yatsopano. Kuti muchite zimenezi, tsatirani malangizo awa:

  1. Tsegulani mu JW Library ku ma Settings kuti muone version yomwe ili m’chipangizo chanu.

  2. Ngati nambala ya version yomwe ili m’chipangizo chanu ndi yaing’ono kuposa ili m’munsiyi, pangani dawunilodi komanso kuika failo ya APK potsatira malangizo ali m’mwambawa.

Version: 11.3.2 (50276)