Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

JW LAIBULALE

Fufuzani M’Baibulo Kapena M’buku pa Zipangizo za Android

Fufuzani M’Baibulo Kapena M’buku pa Zipangizo za Android

Mukhoza kufufuza mawu kapena chiganizo chimene mukufuna m’Baibulo, m’buku ndi zinthu zina pogwiritsa ntchito JW Laibulale.

Kuti muchite zimenezi, tsatirani malangizo ali m’munsiwa:

 Kufufuza M’Baibulo

Mukhoza kufufuza mawu kapena chiganizo m’Baibulo limene mukuwerenga.

Mukamawerenga Baibulo, dinani pabatani lofufuzira (looneka ngati galasi), kenako lembani mawu amene mukufuna kufufuzawo. Mukangoyamba kulemba, muona mawu osiyanasiyana omwe akhoza kukhala amene mukufuna. Mukaona kuti mawu ena omwe abwera akufanana ndi amene mukufuna, adineni kapena dinani batani la Enter kuti muone mavesi amene ali ndi mawuwo.

Mukhozanso kukonza zoti muone mavesi okhawo omwe mumatsegula kawirikawiri amene ali ndi mawu amene mukufunawo (Top Verses), mavesi onse okhala ndi mawuwo (All Verses) kapena mungasankhe kungoona nkhani zakumayambiriro kapena zakumapeto kwa Baibulo zomwe zili ndi mawuwo (Articles).

Ngati mwalemba mawu angapo, dinani pamene palembedwa kuti Match Exact Phrase kuti zotsatira zake zingokhala zokhazo zomwe ndi zofanana ndi zimene mwalembazo.

 Kufufuza M’buku Kapena Chinthu China

Mukhoza kufufuza mawu kapena chiganizo m’buku kapena chinthu china chimene mukuwerenga.

Mukamawerenga buku kapena chinthu china, dinani batani lofufuzira, kenako lembani mawu amene mukufuna kufufuzawo. Mukangoyamba kulemba, muona mawu osiyanasiyana omwe akhoza kukhala amene mukufuna. Mukaona kuti mawu ena omwe abwera akufanana ndi amene mukufuna, adineni kuti mutsegule.

Ngati mwalemba mawu angapo, dinani pamene palembedwa kuti Match Exact Phrase kuti zotsatira zake zingokhala zokhazo zomwe ndi zofanana ndi zimene mwalembazo.

 Kufufuza Mutu

Ngati munapanga dawunilodi buku la Insight on the Scriptures, mukhoza kufufuza mutu womwe uli m’bukuli. Zimenezi zikhoza kutheka mukamawerenga Baibulo, buku kapena chinthu china chilichonse mu JW Laibulale.

Dinani batani lofufuzira, kenako lembani mawu amene mukufuna kufufuzawo. Mukangoyamba kulemba, muona zinthu zina zomwe zikhoza kukhala zimene mukufuna, zomwe zimapezeka m’buku la Insight on the Scriptures. Mukaona kuti mawu ena omwe abwera akufanana ndi amene mukufuna, adineni kapena dinani batani la Enter kuti muone pamene mawuwo akupezeka.

Zimenezi zinayamba kutheka kuyambira mu JW Laibulale 1.3.4 yomwe inatuluka mu October 2014. Laibulaleyi imagwirizana ndi zipangizo zomwe zimagwiritsa ntchito pulogalamu ya Android 2.3 kapena iliyonse yomwe inatuluka pambuyo pake. Ngati mwayesa kuchita zimenezi koma sizikutheka, tsatirani malangizo omwe ali m’nkhani yakuti, “Yambani Kugwiritsa Ntchito JW Laibulale ya pa Zipangizo za Android” pansi pa mutu wakuti Kupeza Zinthu Zatsopano.