Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kuphunzira Chinenero pa JW

Pulogalamu yophunzirira chinenero ya pa JW inakonzedwa ndi a Mboni za Yehova kuti izithandiza anthu amene akuphunzira chinenero kuti azidziwa mawu ambiri a chinenerocho komanso mmene angachilankhulire muutumiki komanso m’misonkhano.

 

Pali Zinenero Zambiri

Sankhani chinenero chimodzi pa zinenero 18 zimene zilipo monga chinenero chimene mukudziwa kapena chimene mukufuna kuphunzira. Mukhoza kusankha Chibengali, Chitchainizi (Chosavuta kumva) ndi mawu ojambulidwa a Chimandarini, Chingelezi, Chifulenchi, Chijeremani, Chihindi, Chiindoneziya, Chitaliyana, Chijapanizi, Chikoleya, Chimyanima, Chipwitikizi, Chirasha, Chisipanishi, Chiswahili, Chitagalogi, Chithai, Chitekishi.

 

Magawo Othandiza Polalikira

Pa pulogalamu yophunzirira chinenero ya pa JW pamapezeka mawu ndi ziganizo zimene zingakuthandizeni polalikira, pophunzitsa komanso pamapezeka mawu otchulidwa Baibulo. Palinso timapepala tambiri ndipo tinaikidwa m’njira yakuti muzitha kufananitsa chinenero chanu ndi chinenero chimene mukuphunziracho.

 

Njira Zophunzirira

  • Kuwerenga: Mungathe kumayerekezera chinenero chanu ndi chimene mukuphunziracho

  • Kumvetsera: Mungathe kumvetsera katchulidwe ka mawu a chinenero chimene mukuphunziracho

  • Kuonera: Mungaonere kavidiyo kakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? ndi kakuti Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji ka m’chinero chimene mukuphunziracho

  • Kwizi: Kukumbukira mawu

 

Zimene Mumakonda

Sungani mawu amene mumakonda kuwagwiritsa ntchito kapena amene amakuvutani kwambiri kuti musamavutike kuwapeza. Mungaonenso mawu amene mumakonda kuwagwiritsa ntchito pagawo lothandiza kukumbukira mawu.

 

Kusintha Mawu a Zinenero Zina

Pulogalamuyi imasintha zilembo za zinenero zovuta kuwerenga kuti zizioneka ndi zilembo za afabeti ya Chingelezi.

 

Ngati Mukufuna Kuthandizidwa

Ngati mukuvutika kugwiritsa ntchito Pulogalamu Yophunzirira Chinenero ya pa JW, lembani ndi kutumiza fomu yomwe mungaipeze pawebusaitiyi kuti muthandizidwe.