Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

JW LIBRARY SIGN LANGUAGE

Mukhoza kuika JW Library Sign Language Pachipangizo cha Android popanda kupita ku App Store

Mukhoza kuika JW Library Sign Language Pachipangizo cha Android popanda kupita ku App Store

Ngati zikukuvutani kuika JW Library Sign Language pa chipangizo chanu cha Android kudzera ku Google Play Store kapena Amazon Appstore, mukhoza kuika nokha pogwiritsa ntchito JW Library Sign Language Android Package Kit (APK).

Chofunika ndi kupita ku ma settings n’kukachonga pamene alemba kuti “install unknown apps” kapena “allow installation from unknown sources.” Kuti mudziwe mmene mungachitire zimenezi mungaone pa malangizo ogwiritsira ntchito chipangizo chanu.

Tsatirani mfundo zotsatirazi kuti muchite dawunilodi komanso kuika JW Library Sign Language APK:

  1. Dinani batani la Download kuti musunge failo ya APK pa chipangizo chanu.

  2. Pezani failo ya APK pa chipangizocho n’kudina kuti muike JW Library Sign Language.

Mukaika JW Library Sign Language APK, muziona nthawi ndi nthawi kuti mudziwe ngati pabwera pulogalamu yatsopano. Kuti mudziwe mmene mungachitire zimenezi, chitani izi:

  1. Tsegulani pa Settings mu JW Library Sign Language ndipo onani kuti ndi version iti imene muli nayo.

  2. Ngati nambala ya version pa chipangizo chanu ndi yochepa kuyerekezera ndi imene ili pa batani lakuti dawunilodi, ndiye kuti muyenera kuchitanso dawunilodi n’kuchita install potsatira mfundo zimene talemba pamwambapa.

Mtundu Wake: 4.2.2 (99021)