Mmene Mungagwiritsire Ntchito iPad, iPhone, ndi iPod touch
Onerani vidiyoyi kuti mudziwe zinthu zosiyanasiyana za pa JW Laibulale zimene zingakuthandizeni. Pezani mayankho amafunso amene anthu amakonda kufunsa okhudza pulogalamuyi.
Zatsopano
March 2026 (Version 15.7)
Malo osonyeza malifalensi m’Baibulo akusonyeza zithunzi zooneka bwino zochokera m’mavidiyo akuti Uthenga Wabwino wa Yesu.
Mavuto ambiri akonzedwa, kuphatikizapo amene amapangitsa kuti pulogalamuyi izingotseka yokha.
December 2025 (Version 15.6)
Gwiritsani ntchito batani lofufuzira limene likupezeka mukadina mawu akuti Library kuti mupeze mabuku, timabuku, mavidiyo, zongomvetsera ndi zinthu zina potengera mutu wake.
Mavuto ambiri akonzedwa, kuphatikizapo amene amapangitsa kuti pulogalamuyi izingotseka yokha.
Pulogalamuyi imalola kuiika m’chipangizo chomwe chili ndi Android 8.0, iOS 15, macOS yokhala ndi chip ya M1 kapena yaposachedwapa, Windows 10 Version 2004 kapena yaposachedwapa.
October 2025 (Version 15.5)
Pulogalamu imakumbukira liwiro la mavidiyo kapena zinthu zanu zongomvetsera ngati munaitseka ikuimba n’kuitsegulanso.
Mukatsegula vidiyo, mutu wa vidiyoyo ndi zina zimabisika. Kuti zionekerenso dinani vidiyoyo.
Mavuto ambiri akonzedwa, kuphatikizapo amene amapangitsa kuti pulogalamuyi izingotseka yokha.
Pulogalamuyi imalola kuiika m’chipangizo chomwe chili ndi Android 7.0, iOS 15, macOS yokhala ndi chip ya M1 kapena yaposachedwapa, Windows 10 Version 2004 kapena yaposachedwapa.
M'CHIGAWO ICHI
Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri Okhudza JW Library (Pa Zipangizo za iOS)
Pezani mayankho a mafunso ofunsidwa kawirikawiri.

