Mmene Mungaigwiritsire Ntchito pa Zipangizo za AndroidTM
Onerani vidiyoyi kuti mudziwe zinthu zosiyanasiyana za pa JW Laibulale zimene zingakuthandizeni. Pezani mayankho amafunso amene anthu amakonda kufunsa okhudza pulogalamuyi.
Zatsopano
March 2026 (Version 15.7)
Malo osonyeza malifalensi m’Baibulo akusonyeza zithunzi zooneka bwino zochokera m’mavidiyo akuti Uthenga Wabwino wa Yesu.
Mavuto ambiri akonzedwa, kuphatikizapo amene amapangitsa kuti pulogalamuyi izingotseka yokha.
December 2025 (Version 15.6)
Gwiritsani ntchito batani lofufuzira limene likupezeka mukadina mawu akuti Library kuti mupeze mabuku, timabuku, mavidiyo, zongomvetsera ndi zinthu zina potengera mutu wake.
Mavuto ambiri akonzedwa, kuphatikizapo amene amapangitsa kuti pulogalamuyi izingotseka yokha.
Pulogalamuyi imalola kuiika m’chipangizo chomwe chili ndi Android 8.0, iOS 15, macOS yokhala ndi chip ya M1 kapena yaposachedwapa, Windows 10 Version 2004 kapena yaposachedwapa.
October 2025 (Version 15.5)
Pulogalamu imakumbukira liwiro la mavidiyo kapena zinthu zanu zongomvetsera ngati munaitseka ikuimba n’kuitsegulanso.
Mukatsegula vidiyo, mutu wa vidiyoyo ndi zina zimabisika. Kuti zionekerenso dinani vidiyoyo.
Mavuto ambiri akonzedwa, kuphatikizapo amene amapangitsa kuti pulogalamuyi izingotseka yokha.
Pulogalamuyi imalola kuiika m’chipangizo chomwe chili ndi Android 7.0, iOS 15, macOS yokhala ndi chip ya M1 kapena yaposachedwapa, Windows 10 Version 2004 kapena yaposachedwapa.
M'CHIGAWO ICHI
Yambani Kugwiritsa Ntchito JW Laibulale ya pa Zipangizo za Android
Dziwani zimene mungachite kuti muzitha kugwiritsa ntchito JW Laibulale pa zipangizo za Android.
Pangani Dawunilodi ndi Kusunga Mabaibulo pa Zipangizo za Android
Dziwani zimene mungachite kuti muzitha kugwiritsa ntchito JW Laibulale pa zipangizo za Android.
Pangani Dawunilodi ndi Kusunga Mabuku pa Zipangizo za Android
Dziwani zimene mungachite kuti muzitha kugwiritsa ntchito JW Laibulale pa zipangizo za Android.
Ikani Kachizindikiro Kokuthandizani Kukumbukira pa Zipangizo za Android
Dziwani zimene mungachite kuti muzitha kuika zizindikiro zokuthandizani kukumbukira mukamawerenga pa zipangizo za Android.
Onani Zimene Munatsegula pa Zipangizo za Android
Dziwani zimene mungachite kuti muzitha kuona zimene munatsegula pa JW Laibulale ya pa zipangizo za Android.
Mukhoza Kusintha Zina ndi Zina Mukamawerenga pa Zipangizo za Android
Dziwani zimene mungachite kuti muzitha kusintha zina ndi zina mukamawerenga pa zipangizo za Android.
Fufuzani M’Baibulo Kapena M’buku pa Zipangizo za Android
Dziwani zimene mungachite kuti muzifufuza mawu kapena ziganizo m’buku la Insight on the Scriptures pa JW Laibulale ya pa zipangizo za Android.
Mukhoza Kuchekenira Mfundo Zofunika pa Zipangizo za Android
Dziwani zimene mungachite kuti muzitha kuchekenira mfundo zofunika pa JW Laibulale yomwe imagwira ntchito pa zipangizo za Android.
Ikani JW Library M’chipangizo cha Android Ngati Simungathe Kupanga Dawunilodi Kudzera pa App Store
Ngati simungathe kuika JW Library kudzera pa app store, mukhoza kuika laibulaleyi pogwiritsa ntchito JW Library Android Package Kit (APK) m’chipangizo chanu.
Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri Okhudza JW Library (Pa Zipangizo za Android)
Pezani mayankho a mafunso ofunsidwa kawirikawiri.

