Pitani ku nkhani yake

JW LIBRARY SIGN LANGUAGE

Zinthu Zopezeka pa JW Library Sign Language

Zinthu Zopezeka pa JW Library Sign Language

Laibulale ya JW ya Chinenero Chamanja

Laibulale ya JW ya Chinenero Chamanja, ndi pulogalamu yovomerezeka ya Mboni za Yehova. Pulogalamuyi imatha kupanga dawunilodi, kuika mavidiyo a chinenero chamanja m’malo oyenera ndi kuwaonetsa pa jw.org.

Onerani mavidiyo a Baibulo komanso mabuku ndi zinthu zina za m’chinenero chamanja. Pangani dawunilodi mavidiyowa n’kuwasunga m’chipangizo chanu cham’manja kuti muzithabe kuonera mukakhala kuti simunalumikize chipangizocho ku Intaneti. Mavidiyowa ali ndi zithunzi zokongola, komanso ndi osavuta kuonera.

 

Ngati Mukufuna Thandizo

Ngati muli ndi funso lokhudza JW Library Sign Language, mnzanu yemwe akuidziwa bwino angathe kukuthandizani. Ngati palibe wokuthandizani, funsani ku ofesi ya nthambi yathu yomwe muli nayo pafupi.