Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Zokuthandizani Pophunzira)

Pangani dawunilodi nkhani zokuthandizani kuphunzirazi ndipo zigwiritseni ntchito pamodzi ndi buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Fufuzani zimene mumakhulupirira, phunzirani zimene Baibulo limaphunzitsa, komanso dziwani mmene mungafotokozere zimene mumakhulupirirazo kwa anthu otsutsa.

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

Bukuli lakonzedwa kuti likuthandizeni pophunzira Baibulo ndipo likufotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani zosiyanasiyana, monga n’chifukwa chiyani timakumana ndi mavuto, kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira, komanso tingatani kuti tikhale ndi banja losangalala.

MUTU 1

Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?—Gawo 1

Kodi mungayankhe bwanji ngati wina atanena kuti, “Kodi Mulungu amalanga anthu oipa powabweretsera mavuto”?

MUTU 1

Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?—Gawo 2

Kodi zingatheke kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu?

MUTU 2

Baibulo ndi Buku Lochokera kwa Mulungu (Gawo 1)

N’chifukwa chiyani tikuti ‘Baibulo ndi buku lochokera kwa Mulungu,’ pamene linalembedwa ndi anthu?

MUTU 2

Baibulo ndi Buku Lochokera kwa Mulungu (Gawo 2)

Pali maumboni ambiri otsimikizira kuti Baibulo ndi lochokeradi kwa Mulungu.

MUTU 3

Kodi Mulungu Ali Nalo Cholinga Chotani Dziko Lapansili? (Gawo 1)

Kodi Mulungu ankafuna kuti zinthu zikhale mmene zililimu?

MUTU 3

Kodi Mulungu Ali Nalo Cholinga Chotani Dziko Lapansili? (Gawo 2)

Ngati Mulungu ankafuna kuti dzikoli likhale Paradaiso, n’chifukwa chiyani panopa lidakali chonchi?

MUTU 3

Kodi Mulungu Ali Nalo Cholinga Chotani Dziko Lapansili? (Gawo 3)

Kodi Mulungu anakonza zoti anthu ndiwo adzathetse mavuto amene ali padzikoli?

MUTU 4

Kodi Yesu Khristu Ndi Ndani? (Gawo 2)

Kodi mungayankhe bwanji munthu atanena kuti Yesu ndi wamkulu mofanana ndi Mulungu?

MUTU 4

Kodi Yesu Khristu Ndi Ndani? (Gawo 3)

Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wolimba mtima komanso wachifundo?

MUTU 5

Dipo la Yesu Ndi Mphatso ya Mulungu Yamtengo Wapatali Kuposa Zonse (Gawo 2)

Kodi imfa ya munthu mmodzi amene anafa zaka masauzande ambiri zapitazo imatikhudza bwanji?

MUTU 6

Kodi Munthu Akafa Amapita Kuti? (Gawo 1)

Kodi akufa amakhalabe ndi moyo kwinakwake? Kodi akuzunzidwa kumoto?

MUTU 6

Kodi Munthu Akafa Amapita Kuti? (Gawo 2)

Kodi Mulungu anatilenga kuti tizikhala ndi moyo kenako n’kufa?

MUTU 8

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani? (Gawo 1)

N’chifukwa chiyani Mulungu anasankha anthu kuti akakhale olamulira m’malo mosankha angelo ambiri omwe ali kumwambako?

MUTU 8

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani? (Gawo 2)

Kodi Ufumu wa Mulungu unachita kale zinthu ziti? Nanga kodi udzachita zotani m’tsogolo?

MUTU 9

Kodi Tilidi ‘M’masiku Otsiriza’? (Gawo 1)

Anthu ena amakayikira zoti tikukhala m’masiku otsiriza. Kodi mumadziwa bwanji kuti mapeto a dzikoli akuyandikira?

MUTU 9

Kodi Tilidi ‘M’masiku Otsiriza’? (Gawo 2)

Baibulo limafotokoza zinthu zabwino zimene zizichitika m’masiku otsiriza ano.

MUTU 10

Mmene Zochita za Angelo Komanso Ziwanda Zimakhudzira Moyo Wathu (Gawo 1)

Kodi angelo alikodi? Kodi pali angelo oipa? Gwiritsani ntchito pepalali kuti mupeze mayankho a mafunsowa.

MUTU 10

Mmene Zochita za Angelo Komanso Ziwanda Zimakhudzira Moyo Wathu (Gawo 2)

Kodi kuyesa kulankhula ndi mizimu n’kulakwa?

MUTU 11

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika? (Gawo 1)

Kodi si zoona kuti zoipa zonse zimene zimachitika amayambitsa ndi Mulungu popeza kuti ndi wamphamvuyonse?

MUTU 11

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika? (Gawo 2)

Malemba amayankha funsoli momveka bwino.

MUTU 12

Khalani ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo (Gawo 2)

Kodi n’zotheka kusangalatsa Mulungu ngakhale kuti Satana amatiyesa?

MUTU 12

Khalani ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo (Gawo 3)

Pamafunika khama kuti munthu akwanitse kukhala ndi makhalidwe ogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Koma kodi n’zothandizadi?

MUTU 13

Muziona Moyo Ngati Mmene Mulungu Amauonera (Gawo 1)

Moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza moyo wathu komanso wa anthu ena?

MUTU 13

Muziona Moyo Ngati Mmene Mulungu Amauonera (Gawo 2)

Gawoli lingakuthandizeni kumvetsa za kagwiritsidwe ntchito ka magazi komanso zimene mumakhulupirira pa nkhani ya kuikidwa magazi. Lingakuthandizeninso kufotokozera anthu ena zimene mumakhulupirira.

MUTU 14

Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala (Gawo 1)

Kodi chofunika kwambiri n’chiyani kuti banja likhale losangalala? Ganizirani mofatsa zimene mumakhulupirira, onani zimene Baibulo limaphunzitsa, komanso onani mmene mungafotokozere zimene mumakhulupirira kwa anthu ena pogwiritsa ntchito zoti muchitezi.

MUTU 14

Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala (Gawo 2)

Kodi makolo ndiponso ana angaphunzirepo chiyani pa chitsanzo cha Yesu? Ganizirani zimene mumakhulupirira komanso zimene Baibulo limanena.

MUTU 15

Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza (Gawo 1)

Kodi zipembedzo zonse zimasangalatsa Mulungu? Ngati si zonse, kodi mungatani kuti mudziwe chipembedzo choona? Fufuzani zimene Baibulo limaphunzitsa ndipo onaninso zimene mumakhulupirira.

MUTU 16

Yesetsani Kuti Muzilambira Mulungu M’njira Yovomerezeka (Gawo 1)

Kodi Mulungu amavomereza kukondwerera tsiku lobadwa, maholide a chipembedzo, komanso kugwiritsa ntchito zifaniziro pomulambira? Kodi Baibulo limati chiyani?

MUTU 18

Ubatizo Umatithandiza Kuti Tikhale pa Ubwenzi ndi Mulungu (Gawo 3)

Kodi Mkhristu amene wadzipereka kwa Mulungu ayenera kutani? Nanga N’chifukwa chiyani anthu amene amakondadi Mulungu ayenera kutsimikiza kuti azichita zinthu mogwirizana ndi kudziperekako pamoyo wawo?