Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

MAVIDIYO OTHANDIZA POPHUNZIRA

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Mabuku a M’Baibulo

Mavidiyowa ali ndi mfundo zokuthandizani kumvetsa nkhani za m’mabuku a m’Baibulo komanso mmene zinthu zinalili pamene bukulo linkalembedwa. Muzigwiritsa ntchito mavidiyowa kuti muzikhala ndi chidwi chowerenga komanso kuphunzira nkhani za m’Baibulo.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Ezara

Yehova anakwaniritsa lonjezo lake pomasula anthu ake ku ukapolo ku Babulo komanso pobwezeretsa kulambira koona ku Yerusalemu.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Nehemiya

Buku la Nehemiya lili ndi mfundo zothandiza anthu onse amene akutumikira Yehova masiku ano.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Esitere

Zinthu zimene zinachitika pa nthawi ya Esitere zikhoza kulimbitsa chikhulupiriro chanu chakuti Yehova Mulungu ali ndi mphamvu yopulumutsa anthu ake akakumana ndi mavuto.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yobu

Anthu onse amene amakonda Yehova adzakumana ndi mayesero. Nkhani ya Yobu imatithandiza kudziwa kuti tikhoza kupitiriza kukhala okhulupirika ndiponso kukhala kumbali ya Yehova.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Masalimo

Buku la Masalimo limasonyeza kuti Yehova ndi woyenera kulamulira. Limathandiza ndiponso kulimbikitsa anthu amene amamukonda komanso limasonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachite posintha zinthu padzikoli.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Miyambo

Pezani malangizo ochokera kwa Mulungu othandiza pa zochitika zosiyanasiyana monga bizinezi komanso mfundo zothandiza mabanja

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Mlaliki

M’bukuli, mfumu Solomo anasiyanitsa zinthu zomwe ndi zofunika kwambiri pa moyo wathu ndi zinthu zimene zimasemphana ndi zomwe Mulungu amafuna.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Nyimbo ya Solomo

Kodi N’chifukwa chiyani bukuli limafotokoza chikondi chenicheni chimene Msulami anasonyeza kwa m’busayo kuti “lawi la Ya”?

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yesaya

Buku la Yesaya lili ndi maulosi olondola omwe angatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova amene ndi Wokwaniritsa malonjezo komanso yemwe ndi Mulungu wa chipulumutso chathu.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yeremiya

Yeremiya anachita utumiki wake mokhulupirika ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto. Onani mmene chitsanzo chake chingathandizire Akhristu masiku ano.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Maliro

Linalembedwa ndi mneneri Yeremiya, buku la Maliro limafotokoza uthenga wachisoni wokhudza kuwonongedwa kwa Yerusalemu komanso kuti kulapa kumachititsa kuti Mulungu atichitire chifundo.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Ezekieli

Ezekieli anadzichepetsa n’kuchita ntchito iliyonse imene Yehova anamuuza kuti achite, ngakhale kuti zinali zovuta. Chitsanzo chake n’chothandiza kwambiri kwa ife masiku ano.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Danieli

Danieli ndi a anzake anakhalabe okhulupirika kwa Yehova pa mayesero onse amene anakumana nawo. Chitsanzo chawo komanso kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’bukuli zimatithandiza ifenso m’masiku otsiriza ano.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Hoseya

Zimene Hoseya analosera zimatiphunzitsa zambiri ponena za mmene Yehova amasonyezera chifundo kwa anthu omwe alapa komanso zimene amafuna kuti tizichita tikamamulambira.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yoweli

Mneneri Yoweli analosera zinthu zomwe zidzachitike pa “tsiku la Yehova” komanso ananena zimene munthu angachite kuti adzapulumuke patsikuli. Ulosi wakewu ndi wofunika kwambiri masiku ano.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Amosi

Yehova anagwiritsa ntchito munthu wodzichepetsayu kuti agwire ntchito yofunika kwambiri. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Amosi?

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Obadiya

Buku la Obadiya ndi lalifupi kwambiri m’Malemba Achiheberi. Bukuli lili ndi uthenga wopereka chiyembekezo komanso limasonyeza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yona

Mneneri Yona analandira chilango chimene Yehova anamupatsa. Bukuli limasonyeza zimene anachita atapatsidwa chilangocho, mmene anachitira utumiki wake komanso mmene Yehova anamuthandizira kudziwa kufunika kokhala wachifundo komanso wokoma mtima. Zimene Yona anakumana nazo zingakuthandizeni kwambiri.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Mika

Ulosi wopezeka m’buku la Mika umatitsimikizira kuti zimene Yehova amayembekezera kwa ife ndi zoti tingazikwanitse komanso zothandiza.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Nahumu

Ulosiwu umatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri zimene Yehova amanena komanso kuti amatonthoza anthu omwe akufunafuna mtendere ndiponso chipulumutso kudzera mu Ufumu wake.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Habakuku

Sitikayikira kuti Yehova amadziwa nthawi yabwino komanso njira yabwino yopulumutsira anthu ake.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Zefaniya

N’chifukwa chiyani tiyenera kumapewa maganizo akuti tsiku la Yehova silidzafika?

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Hagai

Bukuli likusonyeza kufunika koika zinthu zokhudza kulambira Mulungu pamalo oyamba m’moyo wathu.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Zekariya

Masomphenya komanso maulosi ambiri ankalimbikitsa anthu akale. Maulosi amenewa amatitsimikizira kuti Yehova angatithandize ndipo sangatisiye tokha.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Mateyu

Onerani vidiyoyi kuti mudziwe mfundo zina zokhudza bukuli, lomwe ndi buku loyamba la Uthenga Wabwino.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yohane

Buku la Yohane limafotokoza mmene Yesu anasonyezera chikondi chake kwa anthu, chitsanzo chake chabwino cha kudzichepetsa komanso udindo wake wapadera wokhala Mesiya ndiponso Mfumu yam’tsogolo ya Ufumu wa Mulungu.

Onaninso

MABUKU

Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?

Kodi mfundo yaikulu yomwe imapezeka m’Baibulo ndi iti?