Pitani ku nkhani yake

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Kaulukidwe Kodabwitsa ka Ntchentche

Kaulukidwe Kodabwitsa ka Ntchentche

Munthu aliyense amene wayesapo kupha ntchentche amadziwa kuti ndi zovuta kwambiri. Zili choncho chifukwa zimathawa mwamsanga.

Asayansi apeza kuti ntchentche zamtundu winawake zimatha kutembenuka mofanana ndi ndege zankhondo ndipo zimachita zimenezi sekondi imodzi isanathe. Pulofesa wina dzina lake Michael Dickinson ananena kuti ntchentchezi “zikangobadwa kumene zimatha kuuluka mwaukatswiri kwambiri. Zimakhala ngati kakhanda kamene kamabadwa kakudziwa kale kuyendetsa ndege yankhondo.”

Ochita kafukufuku anajambula ntchentchezi zikuuluka ndipo anapeza kuti zimakupiza mapiko awo maulendo 200 pa sekondi iliyonse. Koma zikangokupiza kamodzi zimatha kutembenuka n’kuyamba kuthawa.

Ochita kafukufuku apezanso kuti nthawi imene ntchentchezi zimatenga kuchokera pamene zaona zoopsa kufika poti zithawe ndi yochepa kwambiri moti zingachitike maulendo 50 munthu asanamalize kuphethira. Dickinson ananenanso kuti: “M’kanthawi kochepa kwambiri, ntchentche zimenezi zimazindikira kumene kuli zoopsa n’kudziwa koyenera kuthawira.”

Akatswiri amafunitsitsa kudziwa mmene kaubongo ka ntchentchezi kamachitira zimenezi.

Ntchentchezi zimatha kutembenuka sekondi imodzi isanathe n’kuyamba kuthawa

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti ntchentche zamtunduwu zikhale ndi luso limeneli? Kapena kodi ntchentchezi zinachita kulengedwa?