Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Luso la Maselo Lotha Kugawikana

Luso la Maselo Lotha Kugawikana

 Moyo wanu unayamba ndi kaselo kakang’ono kwambiri koti sikangathe kuoneka ndi maso. Komatu patangopita miyezi ingapo, munabadwa monga mwana wakhanda. Selo limodzilo linachulukana n’kukhala maselo ambirimbiri amitundu yoposa 200, omwe anali osiyana kaonekedwe, kukula komanso ntchito zake.

 Taganizirani izi: Dzira la mayi likakumana ndi umuna wa bambo, limapanga selo limodzi. Selo limeneli limakopera DNA yake n’kugawikana kukhala maselo awiri. Maselo amene apangika amabwereza zimenezi maulendo ambirimbiri. Poyamba, maselo onse atsopanowa amakhala ofanana. Mu DNA yawo mumakhala malangizo onse ofunikira popanga selo la mtundu uliwonse.

 Pakangotha mlungu umodzi kuchokera pamene mayi watenga pathupi, maselo amayamba kugawikana n’kukhala mitundu iwiri. Maselo ena amakhala mluza, pomwe maselo ena amakhala nsengwa ndi tinthu tina tothandiza kuti mluza uzikula.

 Pomafika mlungu wachitatu, maselo a mluza amadzigawa magawo atatu. Maselo a m’gawo lakunja amadzakhala mitsempha, ubongo, pakamwa, khungu komanso maselo ena. Maselo a m’gawo lapakati amadzakhala magazi, mafupa, impso, minofu ndi minyewa ina. Maselo a m’gawo lamkati amadzakhala ziwalo zamkati mwathupi monga mapapo, chikhodzodzo ndiponso zambiri mwa ziwalo zogaya zakudya m’thupi.

Mwana wosabadwa akamakula, maselo amachulukana n’kukhala maselo a mitundu yosiyanasiyana yokwana 200

 Pa nthawi yonse imene mayi ali woyembekezera, maselo amakhala akuyenda kupita mbali zina za mluza, kaya ndi m’magulu kapena limodzilimodzi. Maselo ena amakhala pamodzi n’kupanga zinthu zooneka mosiyanasiyana monga zafulati, zokhala ngati zingwe komanso zokhala ngati matumba. Kuti zimenezi zitheke, maselo amafunika kuchita zinthu mogwirizana kwambiri. Mwachitsanzo, pa nthawi ina maselo omwe apanga zinthu zafulati aja amadzipinda n’kukhala timapaipi ting’onoting’ono. Zimenezi zimachitika m’mbali zosiyanasiyana za mluza pa nthawi imodzi. Kenako timapaipi tija timayamba kutalika komanso kugawikana ndipo pakapita nthawi, timalumikizana n’kukhala mitsempha yonse ya magazi.

 Mwana akamabadwa, maselo ake omwe ndi mabiliyoni mahandiredi ambiri amakhala kuti alipo kale m’mitundu, pamalo ndiponso pa nthawi yoyenera.

 Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti maselo akhale ndi luso lotha kugawikana? Kapena pali winawake amene anawapanga?