Pitani ku nkhani yake

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Luso la Nyerere Lopukuta Tinyanga Take

Luso la Nyerere Lopukuta Tinyanga Take

 Tizilombo tonse timafunika kukhala taukhondo kuti tizitha kuuluka, kuyenda pamalo okwera komanso kuzindikira zinthu zimene zili pafupi. Mwachitsanzo, ngati tinyanga ta nyerere titakhala takuda ndiye kuti singathe kulondola njira, kulankhulana ndi zinzake komanso kumva fungo bwinobwino. N’chifukwa chake wasayansi wina dzina lake Alexander Hackmann ananena kuti “simungapeze kachilombo kosadzisamalira. Tizilombo tonse timadziwa zoyenera kuchita kuti tisade.”

 Taganizirani izi: Hackmann ndi anzake anafufuza zimene nyerere za mtundu winawake (Camponotus rufifemur) zimachita kuti ziyeretse tinyanga take. Anapeza kuti nyererezi zimapinda mwendo m’njira yoti ugwire kanyanga kake n’kupulula tizidutswa ta fumbi kapena zinthu zina. Tiubweya take tolimba timathandiza kuchotsa tizidutswa tokulirapo. Tizidutswa ting’onoting’ono timachotsedwa ndi tiubweya tina tokhala ngati chipeso. Ndiye pali tiubweya tinanso tochepa kwambiri tomwe timachotsa fumbi lochepetsetsa mofanana ndi tsitsi lathu litagawidwa ka 80.

 Vidiyoyi ikusonyeza nyerere ikupukuta tinyanga take

 Hackmann akuona kuti luso la nyerere lopukuta tinyanga take likhoza kuthandiza kwambiri m’mafakitale. Mwachitsanzo, likhoza kuthandiza popukuta tinthu tating’ono timene amagwiritsa ntchito popanga zipangizo chifukwa sitingagwire bwino ntchito ngati titada.

 Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti nyererezi zikhale ndi luso lopukuta tinyanga take? Kapena pali winawake amene anazilenga ndi luso limeneli?