Pitani ku nkhani yake

Dzitetezeni Kuti Musamapusitsidwe ndi Nkhani Zabodza

Dzitetezeni Kuti Musamapusitsidwe ndi Nkhani Zabodza

Masiku ano, mungapeze nkhani ndi mfundo zambiri kuposa kale, kuphatikizapo zokuthandizani kudziteteza komanso kukhala athanzi. Koma pofufuza nkhani, muyenera kusamala ndi izi:

Mwachitsanzo, mliri wa COVID-19 utayamba, mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations anachenjeza kuti nkhani zabodza zafalikira kwambiri. Iye anati: “Malangizo abodza okhudza mankhwala akufala kwambiri. Pa TV komanso wailesi tingamve nkhani zambiri zabodza. Tingapezenso nkhani zosiyasiyana zamphekesera pa intaneti. Komanso pa intaneti anthu akulimbikitsa anzawo kuti azidana ndi anthu ena kapena ndi magulu osiyanasiyana.”

N’zoona kuti nkhani zabodza zakhala zikufala kuyambira kale. Koma Baibulo linalosera kuti m’masiku athu “anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe. Iwo azidzasocheretsa ena ndiponso azidzasocheretsedwa.” (2 Timoteyo 3:1, 13) Chifukwa cha intaneti, panopa timatha kumalandira komanso kufalitsa mosadziwa nkhani zabodza mwamsanga ndiponso mosavuta kuposa kale lonse. Choncho maimelo ndi mamesaji amene timalandira komanso nkhani zimene timawerenga zimakhala ndi mabodza ndi mfundo zambiri zolakwika.

Kodi mungadziteteze bwanji kuti musamapusitsidwe ndi nkhani zabodza komanso zamphekesera? Tiyeni tione mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize.

 • Musamakhulupirire zinthu zonse zimene mumaona ndi kumva

  Zimene Baibulo limanena: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.”—Miyambo 14:15.

  Tikhoza kupusitsidwa mosavuta ngati sitisamala. Mwachitsanzo, taganizirani za mavidiyo afupiafupi kapena zithunzi zokhala ndi mawu ozifotokozera zomwe zimafalitsidwa pa intaneti. Cholinga cha zinthu ngati zimenezi ndi kuseketsa anthu. Koma popeza zinthuzi sizisonyeza nkhani yonse zikhoza kusinthidwa mosavuta. Nthawi zina, anthu amapanga mavidiyo a anthu ena akuchita kapena kunena zinthu zimene sanazichite kapena kuzinena n’komwe.

  “Nthawi zambiri, nkhani zimene anthu ochita kafukufuku amapeza pa intaneti zasinthidwa kapena kupotozedwa.”—Axios Media.

  Dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhaniyi ndi yoona kapena yasinthidwa?’

 • Muziganizira kumene nkhaniyo yachokera komanso zimene imanena

  Zimene Baibulo limanena: “Tsimikizirani zinthu zonse.”—1 Atesalonika 5:21.

  Musanakhulupirire nkhani inayake kapena kuitumiza, ngakhale imene ndi yodziwika kapena imene yalengezedwa pa nyuzi, mutsimikizire kaye kuti ndi yoona. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

  Muziganizira ngati nkhani yachokera kwa munthu kapena kumalo odalirika. Makampani kapena mabungwe ofalitsa nkhani akhoza kusintha nkhanizo chifukwa cha maganizo awo andale kapena okhudza zinthu zina. Muziyerekezera nkhani zochokera kwa ofalitsa nkhani ena ndi nkhani zomwezo zochokera kwa ofalitsa nkhani anzawo. Nthawi zina, anzanu angakutumizireni mamesaji abodza mosadziwa. Choncho musamakhulupirire nkhani iliyonse kusiyapo ngati mungadziwe kumene yachokera.

  Muzitsimikiziranso ngati zimene nkhani imanena n’zatsopano komanso zoona. Muziona madeti, mfundo zotsimikizirika komanso umboni wamphamvu wosonyeza kuti nkhaniyo ndi yoona. Muzisamala kwambiri ngati nkhani ikufotokoza zinthu zovuta m’njira yosavuta kwambiri kapena ngati yalembedwa mokufikirani pamtima kwambiri.

  “Kutsimikizira nkhani n’kofunika kwambiri masiku ano mofanana ndi kusamba m’manja.”—Sridhar Dharmapuri, yemwe amagwira ntchito yoona za zakudya zopatsa thanzi kubungwe la United Nations.

  Dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhaniyi imafotokoza maganizo a anthu ngati kuti ndi mfundo zoona kapena imangofotokoza mbali imodzi?’

 • Muzikhulupirira mfundo zimene n’zoona osati zimene mumangofuna kukhulupirira

  Zimene Baibulo limanena: “Munthu wodalira mtima wake ndi wopusa.”—Miyambo 28:26.

  Anthufe timakonda kukhulupirira zinthu zomwe zimagwirizana ndi zimene tikufuna kukhulupirira. Makampani a intaneti amakonza zinthu kuti tizipeza mosavuta nkhani zimene zimagwirizana ndi zimene timakonda komanso zimene takhala tikufufuza. Koma nthawi zina, zimene timakonda kumva si zimene timafunika kumva.

  “N’zoona kuti anthufe timatha kuganiza bwino. Koma nthawi zambiri zimene timakonda, kufuna komanso kuopa zimachititsa kuti tiziona nkhani zimene zimagwirizana ndi zimene tikufuna kukhulupirira kukhala zoona.”—Peter Ditto, katswiri wa maphunziro a maganizo.

  Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimakhulupirira nkhaniyi chifukwa choti ndikufuna kuikhulupirira basi?’

 • Musamafalitse nkhani zabodza

  Zimene Baibulo limanena: “Usafalitse nkhani yabodza.”—Ekisodo 23:1.

  Muzikumbukira kuti nkhani zimene mungatumize kwa anthu ena zikhoza kukhudza zimene iwo amaganiza komanso kuchita. Ngakhale kuti mwatumiza nkhani zabodza mosadziwa, zotsatirapo zake zingakhale zoipa.

  “Lamulo lofunika n’lakuti muziima kaye n’kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikudziwa kuti nkhaniyi ndi yoona moti ndikhoza kuitumiza kwa ena?’ Ngati aliyense atamachita zimenezi bwenzi nkhani zabodza zimene zimafalitsidwa pa intaneti zikanakhala zochepa kwambiri.”—Peter Adams, wachiwiri kwa woyang’anira ntchito ina yokhudza kufalitsa nkhani.

  Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikutumiza nkhaniyi chifukwa choti ndimadziwa kuti ndi yoona?’