Pitani ku nkhani yake

Zimene Mungachite Ngati Muli Nokhanokha

Zimene Mungachite Ngati Muli Nokhanokha

Kodi muli nokhanokha ndiponso mukusungulumwa? Ngati ndi choncho, mwina mukumva ngati mmene wamasalimo ankamvera pamene anati: “Ndakhala ngati mbalame imene ili yokhayokha padenga.” (Salimo 102:7) M’Baibulo muli mfundo zomwe zingakuthandizeni kulimbana ndi mavuto omwe amabwera chifukwa choti muli nokhanokha.

 Yandikirani Mulungu

Mukhoza kumakhala osangalala ngakhale pamene muli nokhanokha mukazindikira kuti mukufunikira kudziwa Mulungu kenako n’kuyamba kuphunzira za Iye. (Mateyu 5:3, 6) Zinthu zotsatirazi zingakuthandizeni kuchita zimenezi ndipo n’zaulere.

 Werengani mavesi otonthoza m’Baibulo

Anthu ambiri atonthozedwa ndi malembawa. M’malo mowerenga mavesi ambiri nthawi imodzi, gwiritsani ntchito nthawi yomwe muli nokhanokhayo posinkhasinkha nkhani iliyonse payokha komanso popemphera.—Maliko 1:35.

 Dziwani chifukwa chake m’dzikoli mukuchitika zinthu zoipa

 Musamangokhalira kuda nkhawa

Nkhani zotsatirazi zingakuthandizeni kudziwa zimene mungachite kuti muchepetse nkhawa zomwe zimabwera chifukwa chokhala nokhanokha ndiponso zikuthandizani kuti ‘muleke kuda nkhawa.’—Mateyu 6:25.

 Pezani anthu ocheza nawo

Munthu akamacheza ndi ena amachepetsa nkhawa ndiponso amasangalala. Zimenezi n’zofunika kwambiri makamaka pamene simungathe kukumana ndi anzanuwo pamasom’pamaso. Ngati simungathe kuchoka panyumba, mukhoza kumacheza ndi anzanu kudzera pa vidiyokomfelensi kapena kuwaimbira foni kuti mulimbitse ubwenzi wanu komanso kupeza anzanu ena atsopano. Nkhani zotsatirazi zingakuthandizeni kuti mupeze komanso mukhale “bwenzi lenileni.”—Miyambo 17:17.

 Muzichita masewera olimbitsa thupi

Baibulo limavomereza kuti “kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.” (1 Timoteyo 4:8) Kumathandiza kuti muziganiza bwino komanso muzisangalala, makamaka pamene muli nokhanokha. Ngakhale pamene simukuchoka panyumba, pali zinthu zomwe mungachite kuti mulimbitse thupi lanu.