Pitani ku nkhani yake

Kukhala Bwino Ndi Anthu

Kupeza Anzanu

Banja Labwino Komanso Mabwenzi Abwino

Tikhoza kukhala ndi anzathu abwino tikamaganizira kwambiri zimene tingawachitire m’malo mwa zimene iwowo angatichitire.

Kodi Mungatani Kuti Mukhale Bwenzi Labwino?

Anthu ambiri amaona kuti kukhala ndi mabwenzi n’kofunika. Kodi mungatani kuti mukhale bwenzi labwino? Nkhaniyi ikufotokoza mfundo 4 za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni.

Kodi Mnzako Weniweni Ungamudziwe Bwanji?

N’zosavuta kupeza anzanu amene sangakuthandizeni, koma kodi mungapeze bwanji mnzanu weniweni?

Kodi Mungatani Kuti Mukhale ndi Anzanu Apamtima?

Mfundo 4 zomwe zingakuthandizeni kuti mupeze anzanu apamtima.

Kodi Ndiwonjezere Anzanga?

Zimakhala bwino kukhala ndi kagulu kochepa ka anzanu, koma sikuti zimenezi zimathandiza nthawi zonse. N’chifukwa chiyani?

Kusowa Wocheza Naye

Kodi Mungatani Ngati Mumasowa Wocheza Naye

Kusowa ocheza nawo kwa nthawi yaitali kumasokoneza thanzi la munthu mofanana ndi mmene zimakhalira ndi munthu yemwe amasuta ndudu 15 pa tsiku. Kodi mungatani ngati nthawi zina mumaona kuti mumangokhala nokhanokha ndipo mukusowa wocheza naye?

N’chifukwa Chiyani Anzanga Sandikonda?

Si inu nokha amene mukusowa wocheza naye kapena amene mulibe mnzanu. Werengani nkhaniyi kuti muone mmene anthu ena athetsera vutoli.

Ndingatani Ngati Anzanga Amandiona Kuti Ndine Wotsalira?

Kodi mumaona kuti n’zoyenera kuchita zinthu kuti mufanane ndi anzanu omwe satsatira mfundo za makhalidwe abwino kapena mumaona kuti chofunika ndi kungokhala mmene mulili?

Kulankhulana Pazipangizo Zamakono

Zimene Mungachite Kuti Musamagwire Ntchito Pamene Simuli Kuntchito

Mfundo 5 zimene zingakuthandizeni kuti ntchito yanu isamasokoneze banja lanu.

Kodi Mungatani Kuti Zipangizo Zamakono Zisamakusokonezeni?

Zipangizo zamakono zikhoza kulimbitsa kapena kusokoneza banja lanu. Kodi zimenezi zingachitike bwanji?

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani pa Nkhani Yotumizirana Zithunzi pa Intaneti?

Kuika zinthu zimene zimakusangalatsani pa intaneti ndi njira yabwino yolumikizirana ndi anzanu komanso anthu a m’banja lanu, koma kukhoza kukhalanso koopsa.

Muzichita Zinthu Mosamala Mukamacheza ndi Anzanu pa Intaneti

Chitani zinthu mosamala mukamacheza ndi anzanu pa Intaneti.

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Mameseji a Pafoni?

Mameseji a pafoni akhoza kuononga ubwenzi wanu ndi anzanu komanso mbiri yanu. Werengani kuti mudziwe mmene zimenezi zingachitikire

Kodi Mungasonyeze Bwanji Khalidwe Labwino Mukamatumiza ndi Kulandira Mameseji pa Foni?

Kodi mukuona kuti n’kupanda ulemu kusiya kaye kucheza ndi mnzanu kuti muwerenge meseji? Kapena mukuganiza si bwino kumangopitirizabe kucheza ndi mnzanuyo osawerenga kaye meseji imene mwalandira?

Kukhala pa Chibwenzi

Kodi Ndine Wokonzeka Kukhala Pachibwenzi?

Mfundo 5 zimene zingakuthandizeni kudziwa ngati muli wokonzeka kukhala pachibwenzi komanso kulowa m’banja

Kodi Kukopana Kuli Ndi Vuto?

Kodi kukopana n’kutani? N’chifukwa chiyani anthu ena amakopana? Kodi kukopana kuli ndi vuto?

Kodi Ndi Mnzanga Chabe Kapena Amandifuna?​—Gawo 1: Kodi Ndikuona Zizindikiro Zotani?

Nkhaniyi ingakuthandizeni kuti mudziwe ngati munthu amakukondani kapena akungofuna kukhala mnzanu chabe.

Kodi Ndi Mnzanga Chabe Kapena Amandifuna?—Gawo 2: Kodi Ndikumukopa?

Kodi mnzanuyu angaganize kuti mukumufuna chibwenzi? Zimene zingakuthandizeni.

Kodi Ndi Chikondi Chenicheni Kapena Kungotengeka Maganizo?

Onerani vidiyoyi kuti mudziwe tanthauzo la kutengeka maganizo ndiponso chikondi chenicheni.

Kodi Baibulo Limavomereza Kuti Mwamuna ndi Mkazi Azikhalira Limodzi Asanakwatirane?

Malangizo ochokera kwa Mulungu amatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tikhale ndi banja logwirizana ndipo anthu amene amatsatira mfundo zake zinthu zimawayendera bwino nthawi zonse.

Kodi a Mboni za Yehova Amatsatira Mfundo Ziti Zokhudza Kukhala pa Chibwenzi?

Kodi ndi bwino kukhala pa chibwenzi pongofuna kusangalala?

Chikondi Chenicheni

Mfundo za m’Baibulo zingathandize Akhristu posankha munthu woyenera kumanga naye banja, ndiponso zingawathandize kusonyezana chikondi chenicheni akakwatirana.

Kodi Mungatani Ngati Chibwenzi Chatha?

N’chiyani chingakuthandizeni ngati chibwenzi chanu chatha?

Kodi Ndingatani Ngati Chibwenzi Chatha?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungachite ngati mwakhumudwa chifukwa chakuti chibwenzi chatha.

Kuthetsa Mikangano

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupepesa?

Onani zifukwa zitatu zimene muyenera kupepesera ngakhale pamene mukuona kuti simunalakwe chilichonse.

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kukwiya?

Kodi pali zifukwa zomveka zoti munthu angakwiyire? Nanga angatani ngati mkwiyowo wayamba kukula?

Kodi Mungatani Kuti Mugwirizanenso Ngati Mwayambana?

Malangizo a m’Baibulo anathandiza anthu ena kuti ayambe kugwirizana.

Kodi Kukhululuka Kumatanthauza Chiyani?

M’Baibulo muli mfundo 5 zimene zingatithandize kukhululukira ena.

Kodi Mungatani Kuti Muzikhululukirana?

N’chifukwa chiyani kukhululukirana sikophweka? Werengani nkhani kuti muone mmene Baibulo lingakuthandizireni.

Mungatani Kuti Muzikhala Wosangalala?​—Kukhululuka

Munthu amene amakhalira kukwiya komanso kusunga zifukwa, sakhala wosangalala komanso sakhala wathanzi.

Prejudice and Discrimination

Tsankho Likuchitika Padziko Lonse

Kodi tsankho n’chiyani? N’chifukwa chiyani tinganene kuti nthawi zina munthu aliyense amapanga zinthu mwatsankho komanso kuti vuto limeneli lili padziko lonse?

Kodi Muli Ndi Mtima Watsankho?

Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingasonyeze kuti ndife atsankho?

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Kusankhana Mitundu?

Kodi anthu a mitundu yonse ndi ofanana? Kodi kusankhana mitundu kudzatha?

Kodi Tingathetse Bwanji Chidani?​—Muziyesetsa Kupewa Tsankho

Chotsani kamtima koipidwa ndi anthu ena, potengera chitsanzo cha Yehova yemwe ndi wopanda tsankho.

Tsankho​​​—Muzicheza Ndi Anthu Osiyanasiyana

Onani ubwino wocheza ndi anthu omwe mumasiyana nawo zinthu zina.

Kodi N’zotheka Kuti Anthu a Mitundu Yonse Azionedwa Mofanana?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Anthu mamiliyoni akuphunzira kuchokera m’Baibulo mmene angamachitire zinthu mwa ulemu ndi ena.

Kodi Tsankho Lidzatha Liti?

Zitsanzo za anthu ena zimasonyeza kuti Baibulo limathandiza anthu a mitundu yosiyanasiyana kuthana ndi tsankho. Kodi tsankho lidzatha liti?

Kodi Chikondi Komanso Kukhulupirika Zidzagonjetsa Liti Chidani?

N’zovuta kusiya mtima wodana ndi anthu a mtundu wina. Koma taonani zimene Myuda wina komanso munthu wina wa ku Palesitina anachita.

Ndinkafunitsitsa Kuthana ndi Kupanda Chilungamo

Rafika analowa m’gulu la anthu ofuna kuthana ndi zinthu zopanda chilungamo. Koma anaona kuti m’Baibulo muli lonjezo loti ndi Ufumu wa Mulungu wokha womwe udzabweretse mtendere komanso chilungamo padzikoli.