Pitani ku nkhani yake

Kodi Zimene Baibulo Limanena Zokhudza Ukapolo wa Ayuda ku Babulo N’zolondola?

Kodi Zimene Baibulo Limanena Zokhudza Ukapolo wa Ayuda ku Babulo N’zolondola?

Zaka zoposa 2,600 zapitazo, Ayuda anagonjetsedwa n’kutengedwa ndi a Babulo, ndipo anakakhala akapolo kwa zaka pafupifupi 70. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anali ataneneratu za mmene moyo wa Ayuda udzakhalire ku ukapoloko. Anawauza kuti: “Mangani nyumba ndi kukhalamo. Limani minda ndi kudya zipatso zake. Tengani akazi ndipo mubereke ana aamuna ndi aakazi. . . . Komanso mzinda umene ndakuchititsani kukhalamo monga akapolo, muziufunira mtendere.” (Yeremiya 29:1, 4-7) Kodi ndi mmenedi zinthu zinalili pa moyo wa Ayuda?

Ochita kafukufuku anagwiritsa ntchito mapale oposa 100 omwe ayenera kuti anali a ku Babulo kapena mizinda ina yapafupi. Zimene zinalembedwa pa mapalewa zikusonyeza kuti ku ukapoloko Ayuda ankatsatirabe zikhalidwe zawo komanso sanasiye chipembedzo chawo. Ngakhale zinali choncho iwo ankagonjera ulamuliro wa a Babulo. Pamapale omwe anapezeka mu 572 mpaka 477 B.C.E, panalembedwanso nkhani zokhudza kuchititsa lendi zinthu, mabizinezi komanso maumboni osainidwa bwino okhudza nkhani zina za ndalama. Buku lina limanena kuti: “Mapale omwe anapezekawa amatithandiza kudziwa mmene moyo unalili kwa akapolowa. Iwo ankakhala moyo wofanana ndi wa munthu aliyense wakumudzi. Iwo ankalima minda, ankamanga nyumba, ankapereka misonkho ndiponso ankachita zinthu zina zomwe mfumu yawalamula.”

Phale la ku Judahtown

Zimene ofufuza anapeza zimasonyezanso kuti panali dera lina lotchedwa Al Yahudu kapena kuti Judahtown komwe Ayuda ambiri ankakhala. Pamapalewa panalembedwa mayina Achiyuda a mibadwo 4 ndipo mayina ena anali a m’Chiheberi. Mapalewa asanapezeke, akatswiri a maphunziro sankadziwa zambiri zokhudza mmene moyo wa Ayuda unalili pa nthawi imene anali akapolo ku Babulo. Dr. Filip Vukosavović, a m’bungwe la Israel Antiquities Authority ananena kuti: “Mapalewa atithandiza kudziwa bwino zokhudza Ayuda omwe anali ku ukapolowa, mayina awo, kumene ankakhala, nthawi imene anakhalapo komanso zomwe ankachita.”

Ayuda omwe anali akapolo ku Babulo ankakhala mwamtendere

Ayuda ali ku ukapolo anali ndi ufulu wochita zinthu zimene akufuna, kuphatikizapo kukhala malo alionse omwe akufuna. A Vukosavović ananena kuti sikuti Ayudawo “ankangokhala ku Al-Yahudu kokha, koma ankapitanso kukakhala m’mizinda ina yosiyanasiyana.” Ena anaphunzira maluso a ntchito zosiyanasiyana ndipo patapita nthawi, anadzagwiritsa ntchito malusowo pomanganso Yerusalemu. (Nehemiya 3:8, 31, 32) Mapale omwe anapezeka ku Al-Yahudu amasonyeza kuti panali Ayuda ena omwe anasankha kukhalabe ku Babulo ngakhale kuti ukapolo unali utatha. Zimenezi zikusonyeza kuti Ayuda omwe anali ku ukapolo ku Babulo ankakhala mwamtendere, ngati mmene Mawu a Mulungu ananenera kale.