Pitani ku nkhani yake

N’chifukwa Chiyani Baibulo Limati Yesu Ndi Mwana wa Mulungu?

N’chifukwa Chiyani Baibulo Limati Yesu Ndi Mwana wa Mulungu?

Yankho la m’Baibulo

 Nthawi zambiri Baibulo limatchula Yesu kuti ndi “Mwana wa Mulungu.” (Yohane 1:49) Mawu akuti “Mwana wa Mulungu,” akusonyeza kuti Mulungu ndiye Mlengi, Kasupe wa zamoyo zonse kuphatikizaponso Yesu. (Salimo 36:9; Chivumbulutso 4:11) Baibulo silinena kuti Mulungu anaberekadi mwana ngati mmene zimakhalira ndi anthu.

 Baibulo limatchulanso angelo kuti ndi “ana a Mulungu woona.” (Yobu 1:6) Limanenanso kuti munthu woyambirira Adamu, anali “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Komabe, popeza kuti Yesu ndi woyambirira kulengedwa komanso kuti analengedwa ndi Mulungu weniweniyo, Baibulo likamanena za Yesu limati ndi Mwana wokondedwa kwambiri wa Mulungu.

 Kodi n’zoona kuti Yesu ankakhala kumwamba asanabadwe padziko pano?

 Inde. Yesu anali cholengedwa chauzimu asanabwere kudzabadwa ngati munthu padziko lapansi pano. Ndipo Yesuyo ananena kuti: “Ndinatsika kuchokera kumwamba.”—Yohane 6:38; 8:23.

 Mulungu analenga Yesu asanalenge china chilichonse. Baibulo limanena za Yesu kuti:

  •   “Iye ndiye . . . woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.”—Akolose 1:15.

  •   Ndi “woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.”—Chivumbulutso 3:14.

 Yesu anakwaniritsa ulosi wonena za ‘munthu amene wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira, [amene] wakhala alipo kuyambira masiku akalekale.’—Mika 5:2; Mateyu 2:4-6.

 Kodi Yesu ankagwira ntchito yanji asanabwere padzikoli?

 Anali ndi udindo wapamwamba. Yesu ankanena za udindo umenewu pamene anapemphera kuti: “Atate, . . . mundipatse ulemerero umene ndinali nawo pambali panu dziko lisanakhalepo.”—Yohane 17:5.

 Ankathandiza Atate ake kulenga zinthu zonse: Yesu ankagwira ntchito limodzi ndi Mulungu monga “mmisiri waluso.” (Miyambo 8:30) Ponena za Yesu, Baibulo limanena kuti: “Chifukwa kudzera mwa iye zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi.”—Akolose 1:16.

 Mulungu anagwiritsa ntchito Yesu polenga china chilichonse kuphatikizapo angelo, ngakhalenso zinthu zomwe timaziona m’chilengedwechi. (Chivumbulutso 5:11) Tinganene kuti Mulungu ndi Yesu anachita zinthu mogwirizana, ngati mmene zimakhalira pakati pa munthu waluso lojambula mapulani a nyumba ndi mmisiri womanga nyumba. Munthu waluso amajambula pulani ya nyumba, pamene mmisiri ndi amene amamanga nyumbayo potsatira pulaniyo.

 Ankatumikira monga Mawu. Baibulo limanena kuti Yesu asanakhale munthu, ankatchedwa kuti “Mawu.” (Yohane 1:1) Izi zikusonyeza kuti Mulungu ankagwiritsa ntchito Yesu kuti apereke uthenga komanso malangizo kwa angelo ena.

 Zikuonekanso kuti nthawi zina Yesu ankagwira ntchito monga Womulankhulira Mulungu akafuna kulankhula ndi anthu padziko lapansi pano. N’kuthekanso kuti Mulungu anagwiritsa ntchito Yesu monga Mawu popereka malangizo kwa Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni. (Genesis 2:16, 17) Akhozanso kukhala Yesu yemweyo amene anali mngelo wotsogolera Aisiraeli m’chipululu ndipo Aisiraeliwo ankayenera kumvera mawu ake onse.—Ekisodo 23:20-23. a

a Mulungu ankagwiritsanso ntchito angelo ena akafuna kulankhula ndi anthu, osati Mawu yekha. Mwachitsanzo, Mulungu anagwiritsa ntchito angelo ena, osati Mwana wake Woyamba Kubadwa, popereka Chilamulo kwa Aisiraeli.—Machitidwe 7:53; Agalatiya 3:19; Aheberi 2:2, 3.