Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

N’chifukwa Chiyani Yesu Amatchedwa Mwana wa Mulungu?

N’chifukwa Chiyani Yesu Amatchedwa Mwana wa Mulungu?

Yankho la m’Baibulo

Mulungu alibe mkazi weniweni amene amabereka ana ake. Koma Mulungu ndiye analenga zinthu zonse kuphatikizapo zamoyo. (Chivumbulutso 4:11) Motero Adamu, amene ndi munthu woyambirira kulengedwa ndi Mulungu, amatchedwa “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Baibulo limaphunzitsanso kuti Yesu analengedwa ndi Mulungu, n’chifukwa chake amatchedwa “Mwana wa Mulungu.”—Yohane 1:49.

Mulungu analenga Yesu asanalenge Adamu. Ponena za Yesu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Iye ndiye chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo, woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” (Akolose 1:15) Yesu anali alipo kale kumwamba asanabadwe padziko lapansi ku Betelehemu. Ndipotu Baibulo limanena kuti “munthu ameneyu wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira, wakhala alipo kuyambira masiku akalekale.” (Mika 5:2) Monga mwana woyamba kubadwa wa Mulungu, Yesu analipo kale kumwamba ndipo anali ndi thupi lauzimu asanabadwe padziko lapansi pano monga munthu. Ndipotu Yesu anachita kunena yekha kuti: “Ndinatsika kuchokera kumwamba.”—Yohane 6:38; 8:23.