Pitani ku nkhani yake

Kodi Yerusalemu Watsopano N’chiyani?

Kodi Yerusalemu Watsopano N’chiyani?

Yankho la m’Baibulo

Mawu akuti “Yerusalemu Watsopano” amapezeka maulendo awiri m’Baibulo. Mawuwa omwe amayerekezeredwa ngati mzinda, amaimira gulu la otsatira a Yesu amene adzalamulire naye limodzi kumwamba mu Ufumu wa Mulungu. (Chivumbulutso 3:12; 21:2) M’Baibulo, gululi limatchedwanso mkwatibwi wa Khristu.

Mfundo zotithandiza kudziwa bwino za Yerusalemu Watsopano

  1. Yerusalemu Watsopano ali kumwamba. Nthawi zonse Baibulo likamanena za Yerusalemu Watsopano, limasonyeza kuti ndi mzinda womwe ukutsika kuchokera kumwamba. Limatinso angelo ndi amene amalondera zipata zake. (Chivumbulutso 3:12; 21:2, 10, 12) Baibulo limasonyeza kuti mzindawu ndi waukulu kwambiri moti sungakwane padziko lapansili. Limati mzindawu ndi wokwana “masitadiya 12,000,” m’litali komanso m’lifupi. * (Chivumbulutso 21:16) Mbali zake zonse zinali zazitali pafupifupi makilomita 560 kupita m’mwamba.

  2. Yerusalemu Watsopano anapangidwa ndi gulu la otsatira a Yesu, omwe ali ngati mkwatibwi wa Khristu. Yerusalemu Watsopano amatchedwa kuti “mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 21:9, 10) Palembali, Mwanawankhosa akuimira Yesu Khristu. (Yohane 1:29; Chivumbulutso 5:12) Ndipo “mkazi wa Mwanawankhosa” yemwe ndi mkwatibwi wa Khristu, akuimira Akhristu odzozedwa amene akakhale ndi Yesu kumwamba. Baibulo limasonyeza kuti Yesu ndi Akhristu odzozedwawa ndi ogwirizana ngati mmene zimakhalira pakati pa mwamuna ndi mkazi wake. (2 Akorinto 11:2; Aefeso 5:23-25) Kuwonjezera pamenepo, pamiyala yomangira maziko a mzinda wa Yerusalemu Watsopano, panalembedwa “mayina 12 a atumwi 12 a Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 21:14) Mfundo imeneyi ikutithandiza kudziwa bwino amene ali m’gulu la Yerusalemu Watsopano. Tikutero chifukwa chakuti Akhristu amene amaitanidwa kuti akakhale kumwamba amapangidwa kuchokera “pamaziko a atumwi ndi aneneri.”​—Aefeso 2:20.

  3. Yerusalemu Watsopano ndi mbali ya boma lakumwamba. Mzinda wakale wa Yerusalemu unali likulu la ku Isiraeli, kumene Mfumu Davide, mwana wake Solomo komanso ana awo analamulira “pampando wachifumu wa Yehova.” (1 Mbiri 29:23) Mzinda wa Yerusalemu unkatchedwa kuti “mzinda woyera,” chifukwa anthu a m’banja la Davide omwe ankalamulira ngati mafumu, ankaimira Ufumu wa Mulungu. (Nehemiya 11:1) Yerusalemu Watsopano yemwenso amatchedwa kuti “mzinda woyera,” wapangidwa ndi Akhristu omwe adzakhale ndi Yesu kumwamba ndipo “adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.”​—Chivumbulutso 5:9, 10; 21:2.

  4. Yerusalemu Watsopano adzathandiza anthu okhala padziko lapansi kuti adzapeze madalitso. Baibulo limanena kuti mzinda wa Yerusalemu Watsopano “ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu.” Izi zikusonyeza kuti Mulungu amagwiritsanso ntchito mzindawu pofuna kukwaniritsa zinthu zina padzikoli. (Chivumbulutso 21:2) Mawu a pavesili akusonyeza kuti pali kufanana pakati pa Yerusalemu Watsopano ndi Ufumu wa Mulungu womwe udzachititse kuti chifuniro cha Mulungu chichitike “monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Madalitso ena omwe Mulungu adzapereke kwa anthu padzikoli ndi monga:

    • Kuchotsa uchimo. Baibulo limanena kuti “mtsinje wa madzi a moyo,” ukuyenda kuchokera ku Yerusalemu Watsopano ndipo ukuthirira “mitengo ya moyo” yokhala ndi masamba “ochiritsira mitundu ya anthu.” (Chivumbulutso 22:1, 2) Kuchiritsa kumeneku komwe kukuimiranso kuchotsa matenda enieni, kudzachotsa uchimo ndipo zimenezi zidzachititsa kuti anthu akhalenso angwiro ngati mmene Mulungu ankafunira poyamba.​—Aroma 8:21.

    • Kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Uchimo unachititsa kuti titalikirane ndi Mulungu. (Yesaya 59:2) Choncho uchimo ukadzachotsedwa, lonjezo la pa Chivumbulutso 21:3 lidzakwaniritsidwa. Lonjezoli limati: “Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo.”

    • Imfa komanso mavuto onse zidzatha. Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pochotsa mavuto onse ndipo “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”​—Chivumbulutso 21:4.

^ ndime 5 Sitadiya, unali mlingo wa Aroma woyezera kutalika kwa malo ndipo sitadiya imodzi inali yofanana ndi mamita 185.