Pitani ku nkhani yake

Kodi Ulosi Umatanthauza Chiyani?

Kodi Ulosi Umatanthauza Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

Ulosi ndi uthenga wochokera kwa Mulungu wopita kwa anthu. Baibulo limanena kuti aneneri “analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.” (2 Petulo 1:20, 21) Apa zikusonyeza kuti mneneri ndi munthu amene amalandira uthenga kuchokera kwa Mulungu n’kumauza anthu ena.​—Machitidwe 3:18.

Kodi aneneri ankalandira bwanji mauthenga ochokera kwa Mulungu?

Mulungu anagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana popereka mauthenga kwa aneneri ake:

  • Kulemba. Mulungu anagwiritsa ntchito njira imeneyi pamene analemba Malamulo Khumi ndi kuwapereka kwa Mose.​—Ekisodo 31:18.

  • Kulankhula kudzera mwa angelo. Mwachitsanzo, Mulungu anagwiritsa ntchito mngelo pouza Mose uthenga woti akapereke kwa Farao ku Iguputo. (Ekisodo 3:2-4, 10) Mulungu akafuna kuti uthenga wake ukhale ndi mawu ena apadera, ankauza angelo kuti akafotokozere anthu uthengawu ndendende mmene iyeyo waunenera. Mwachitsanzo anachita zimenezi pa nthawi imene anauza Mose kuti: “Dzilembere mawuwa chifukwa ine ndikuchita pangano ndi iwe ndi Isiraeli mogwirizana ndi mawu amenewa.”​Ekisodo 34:27. *

  • Masomphenya. Nthawi zina mneneri ankaona masomphenya ali m’maso komanso akudziwa zimene zikuchitika. (Yesaya 1:1; Habakuku 1:1) Masomphenya ena ankaoneka ngati ndi zenizeni moti anthu amene anaonetsedwa masomphenyawo ankachita zinthu ngati kuti zikuchitikadi. (Luka 9:28-36; Chivumbulutso 1:10-17) Koma nthawi zina aneneri ankaona masomphenya atachita ngati akomoka. (Machitidwe 10:10, 11; 22:17-21; Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Mulungu ankatumizanso uthenga wake kwa aneneri pogwiritsa ntchito maloto aneneriwo ali m’tulo.​—Danieli 7:1; Machitidwe 16:9, 10.

  • Kutsogolera maganizo awo. Mulungu ankatsogolera maganizo a aneneri ake kuti iwo azindikire uthenga wake. Izi n’zogwirizana ndi mawu a m’Baibulo akuti: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” Mawu amene anamasuliridwa kuti ‘kuuzira’ akhoza kumasuliridwanso kuti ‘kupumira.’ (2 Timoteyo 3:16; The Emphasised Bible) Choncho zinali ngati Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera, kapena kuti mphamvu imene amagwiritsa ntchito, kuti apumire uthenga wake m’maganizo mwa atumiki ake. Ndiyeno aneneriwo akalandira uthenga wochokera kwa Mulungu, ankasankha mawu abwino oti agwiritse ntchito poulemba.​—2 Samueli 23:1, 2.

Kodi nthawi zonse ulosi umaneneratu zam’tsogolo?

Ayi, sikuti maulosi onse a m’Baibulo amangonena zam’tsogolo zokha. Koma n’zoona kuti mauthenga ambiri ochokera kwa Mulungu amanena zinazake zokhudza m’tsogolo. Mwachitsanzo, kawirikawiri aneneri a Mulungu ankachenjeza Aisiraeli chifukwa cha makhalidwe awo oipa. Aneneriwo ankafotokoza madalitso amene Aisiraeliwo angalandire akamvera chenjezolo komanso tsoka limene angakumane nalo akapanda kumvera. (Yeremiya 25:4-6) Zotsatirapo zake zinkadalira zimene Aisiraeliwo angasankhe kuchita.​—Deuteronomo 30:19, 20.

Zitsanzo za maulosi a m’Baibulo omwe sananeneretu zam’tsogolo

  • Nthawi ina Aisiraeli atapempha kuti Mulungu awathandize, iye anatuma mneneri kuti akawauze zoti Mulungu sanawathandize chifukwa choti sanamvere malamulo ake.​—Oweruza 6:6-10.

  • Pamene Yesu ankalankhula ndi mayi wachisamariya, ananena zinthu zokhudza mbiri ya mayiyo zomwe Yesuyo sakanazidziwa popanda kuuzidwa ndi Mulungu. Mayiyo anazindikira kuti Yesu anali mneneri ngakhale kuti sananeneretu chilichonse cham’tsogolo.​—Yohane 4:17-19.

  • Pa nthawi imene anthu ankaimba Yesu mlandu, adani ake anamuphimba kumaso, kumumenya ndi kumuuza kuti: “Losera. Wakumenya ndani”? Apa sikuti adaniwo ankafuna kuti Yesu anene zam’tsogolo koma kuti, mothandizidwa ndi Mulungu, anene amene wamumenya.​—Luka 22:63, 64.

^ ndime 7 Ngakhale kuti m’chitsanzochi zingaoneke kuti Mulungu ndi amene analankhula ndi Mose, Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anagwiritsa ntchito angelo popereka Chilamulo kwa Mose.​—Machitidwe 7:53; Agalatiya 3:19.