Pitani ku nkhani yake

Kodi Yesu Atafa Anakulungidwa mu Nsalu ya Maliro Yomwe Inasungidwa ku Turin?

Kodi Yesu Atafa Anakulungidwa mu Nsalu ya Maliro Yomwe Inasungidwa ku Turin?

Yankho la m’Baibulo

Baibulo silinena chilichonse chokhudza nsalu ya maliro yomwe imasungidwa ku Turin. Ambiri amaganiza kuti nsaluyi ndi imene anakulungiramo Yesu Khristu pomuika m’manda. Chifukwa cha zimenezi, anthu ena amaona kuti nsaluyi ndi chimodzi mwa zinthu zopatulika kwambiri pa chipembedzo chachikhristu. Panopa nsaluyi ili ku tchalitchi cha katolika ku Turin, m’dziko la Italy ndipo inasungidwa m’bokosi lapamwamba lotetezeka kwambiri.

Kodi mfundo za m’Baibulo zimasonyeza kuti Yesu anakulungidwadi mu nsalu ya ku Turin? Ayi.

Tiyeni tione zinthu zitatu zomwe zikusonyeza kuti nsaluyi si imene inatchulidwa m’Baibulo.

 1. Nsalu ya maliro ya ku Turin ndi yaitali masentimita 442 m’litali komanso masentimita 113 m’lifupi ndipo ili ndi kachigamba ka masentimita 8 komwe kanawonjezeredwa m’litali mwake.

  Zimene Baibulo limanena: Thupi la Yesu linakulungidwa mu nsalu zingapo osati imodzi ndipo mutu wake anaukulunganso ndi nsalu ina. Yesu ataukitsidwa, mmodzi wa ophunzira ake anafika kumanda ake ndipo anapeza “nsalu zokulungira mtembozo zili pansi.” Baibulo limanenanso kuti ‘nsalu ina imene anamukulungira kumutu anaipindapinda ndi kuiika payokha. Imeneyi sinaikidwe pamodzi ndi nsalu zokulungira mtembozo.’—Yohane 20:6, 7.

 2. Nsalu ya maliro ya ku Turin ndi yothimbirira ndipo imaoneka kuti inathimbirira chifukwa cha magazi a mtembo womwe sunasambitsidwe.

  Zimene Baibulo limanena: Yesu atamwalira, ophunzira ake anakonza thupi lake “malinga ndi mwambo umene Ayuda anali kutsatira.” (Yohane 19:39-42) Mwambowu unkaphatikizapo kusambitsa mtembowo, kuupaka mafuta ndi zinthu zina zonunkhiritsa usanakaikidwe m’manda. (Mateyu 26:12; Machitidwe 9:37) Choncho n’zoonekeratu kuti ophunzira ake ayenera kuti anayamba kaye asambitsa mtembo wake asanaukulunge munsalu.

 3. Nsalu ya maliro ya ku Turin inadindikira chithunzithunzi cha munthu. Buku lina linanena kuti: chithunzicho chimasonyeza kuti mtembo wa munthuyo “unagonekedwa mbali imodzi ya m’litali mwa nsaluyo. Ndipo mbali ina ya nsaluyo, anaiwonjezera nsalu ina yaikulu ngati yomweyi chakumutu kwake kuti aziphimbira mtembowo.”—Encyclopædia Britannica.

  Zimene Baibulo limanena: Yesu atafa, nthawi ina ophunzira ake anakambirana za kumwalira kwake, za kusowa kwa mtembo wake m’manda komanso za azimayi omwe anaona ‘masomphenya a angelo, amene anawauza kuti iye ali ndi moyo.’ (Luka 24:15-24) Ngati nsalu ya ku Turin ndi yomwe inapezekadi m’manda a Yesu, n’zosakayikitsa kuti ophunzira ake akanakambirananso za nsaluyo komanso za chithunzi chomwe chinadindika pansalupo. Koma Baibulo silifotokoza ngati ophunzirawo anakambiranako zimenezi.

Kodi n’zoyenera kulemekeza nsaluyi?

Ayi. Ngakhale zikanakhala kuti ndi zoona kuti Yesu anakulungidwadi munsaluyo, kuilemekeza kukanakhalabe kolakwika. Tiyeni tione mfundo za m’Baibulo zomwe zikutichititsa kunena zimenezi.

 1. Si chinthu chofunika. Yesu ananena kuti: “Mulungu ndiye Mzimu, ndipo onse omulambira ayenera kumulambira motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.” (Yohane 4:24) Kulambira kovomerezeka kwa Mulungu sikumafuna kugwiritsa ntchito zizindikiro zachipembedzo.

 2. Ndi zosavomerezeka: Kale, Malamulo Khumi sankalola kuti anthu azilambira mafano. (Deuteronomo 5:6-10) Baibulo limalamulanso Akhristu kuti: “Pewani mafano.” (1 Yohane 5:21) Anthu ena akhoza kunena kuti nsalu ya maliro ya ku Turin, ndi chizindikiro cha chipembedzo chawo basi, osati fano. Komabe, ngati munthu amalemekeza kwambiri chinthu kapena chizindikiro chinachake, ndiye kuti ndi fano lake. * Choncho, munthu amene akufuna kuti Mulungu azisangalala naye sayenera kudzipereka kapena kulemekeza chizindikiro china chilichonse, kuphatikizapo nsalu ya maliroyi.

^ ndime 15 Fano likhoza kukhala chithunzi, chifaniziro kapena chizindikiro chilichonse chomwe anthu angachigwiritse ntchito polambira.