Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

N’chifukwa Chiyani Mulungu Sayankha Mapemphero Ena?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Sayankha Mapemphero Ena?

Yankho la m’Baibulo

 Mulungu sayankha mapemphero ena. Taonani mfundo ziwiri zotsatirazi zimene zimachititsa kuti Mulungu asayankhe mapemphero a anthu ena.

1. Kupempha zinthu zosagwirizana ndi zimene Mulungu akufuna

 Mulungu sayankha mapemphero osagwirizana ndi mfundo zake zimene zili m’Baibulo. (1 Yohane 5:14) Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti tiyenera kupewa mtima wadyera. Juga imalimbikitsa mtima wadyera. (1 Akorinto 6:9, 10) Choncho, Mulungu sangayankhe ngati mukupemphera kuti muwine pa mpikisano kapena juga. Mulungu samangochita chilichonse chimene munthu amafuna. Ndipotu tiyenera kuyamikira zimenezi. Izi zili choncho chifukwa bwenzi tikuopa kuti anthu ena angathe kumupempha ali ndi zolinga zoipa.—Yakobo 4:3.

2. Ngati amene akupempherayo samvera Mulungu mwadala

 Mulungu samayankha mapemphero a anthu amene amachita zoipa mwadala. Mwachitsanzo, Mulungu anauza anthu amene ankati akumutumikira koma samumvera mwadala, kuti: “Ngakhale mupereke mapemphero ambiri, ine sindimvetsera. Manja anu adzaza magazi amene mwakhetsa.” (Yesaya 1:15) Koma anthuwo akanasiya zoipa zomwe ankachita n’kukonza ubwenzi wawo ndi Mulungu, iye akanayamba kumvetsera mapemphero awo.—Yesaya 1:18.