Pitani ku nkhani yake

N’chifukwa Chiyani Mtendere Ndi Wosowa M’dzikoli?

N’chifukwa Chiyani Mtendere Ndi Wosowa M’dzikoli?

Yankho la m’Baibulo

 Ngakhale kuti anthu akhala akuyesetsa kuti abweretse mtendere padziko lapansili, iwo alephera. Ngakhale m’tsogolo muno, anthu sadzakwanitsa kubweretsa mtendere. Izi zili choncho pa zifukwa zotsatirazi:

  •   “Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Anthu sanalengedwe m’njira yoti angathe kudzilamulira okha, choncho sangathe kubweretsa mtendere weniweni padzikoli.

  •   “Musamakhulupirire anthu olemekezeka, kapena mwana wa munthu wina aliyense wochokera kufumbi amene alibe chipulumutso. Mzimu wake umachoka, ndipo iye amabwerera kunthaka. Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.” (Salimo 146:3, 4) Atsogoleri a mayiko, ngakhale amene amafunitsitsadi kukonza zinthu, sangathe kuchotseratu zinthu zomwe zimayambitsa nkhondo.

  •   “Koma dziwa kuti, masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala . . . oopsa, osakonda zabwino, achiwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada.” (2 Timoteyo 3:1-4) Ifeyo tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ a dziko loipali ndipo anthu ambiri ali ndi makhalidwe oipa zedi. Zimenezi zikuchititsa kuti mtendere ukhale wovuta kuupeza.

  •   “Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chivumbulutso 12:12) Mdyerekezi, yemwe ndi mdani wa Mulungu, anaponyedwa kudzikoli ndipo akuchititsa anthu kuti azitengera mtima wake woipa. Ndipo pa nthawi yonse imene iye akhalebe “wolamulira wa dzikoli,” sizingatheke kuti anthu azikhala mwamtendere.—Yohane 12:31.

  •   “[Ufumu wa Mulungu] udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo [otsutsana ndi Mulungu], ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.” (Danieli 2:44) Choncho, ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzabweretse mtendere weniweni womwe anthu akuulakalaka, osati boma linalake la anthu.—Salimo 145:16.