Pitani ku nkhani yake

Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo Ndi Ndani?

Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo Ndi Ndani?

Yankho la m’Baibulo

Mikayeli, amene anthu a zipembedzo zina amamutchula kuti “Mikayeli Woyera,” ndi dzina la Yesu lomwe wakhala akuligwiritsa ntchito asanabwere padziko lapansi komanso atabwerera kumwamba. * Pa nthawi ina, Mikayeli anakangana ndi Satana za mtembo wa Mose. Pa nthawi inanso, Mikayeli anathandiza mngelo wina yemwe anatumidwa kuti akapereke uthenga wa Mulungu kwa mneneri Danieli. (Danieli 10:13, 21; Yuda 9) Dzina lakuti Mikayeli limatanthauza kuti, “Ndani Ali Ngati Mulungu?” Mikayeli wakhala akuchita zinthu mogwirizana ndi dzina lakeli chifukwa amateteza ulamuliro wa Mulungu komanso amamenya nkhondo polimbana ndi adani a Mulungu.​—Danieli 12:1; Chivumbulutso 12:7.

Tiyeni tione chifukwa chake tikunena kuti Mikayeli mkulu wa angelo, ndi Yesu.

  • Mikayeli ndi “mkulu wa angelo.” (Yuda 9) Mawu akuti “mkulu wa angelo,” amatchulidwa m’mavesi awiri okha m’Baibulo. Mavesi awiri onsewa amagwiritsa ntchito mawu osonyeza kuti mngelo amene ali ndi udindo umenewu, ndi mmodzi. Limodzi mwa mavesi amenewa, likusonyeza kuti Ambuye Yesu “adzatsika kumwamba, ndi mfuu yolamula ya mawu a mkulu wa angelo.”(1 Atesalonika 4:16) Choncho, chifukwa chakuti Baibulo likunena kuti Yesu ali ndi mawu a mkulu wa angelo, zimenezi zikusonyeza kuti Mikayeli mkulu wa angelo, ndi Yesu.

  • Mikayeli amatsogolera gulu la nkhondo la angelo. “Mikayeli ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka,” chomwe ndi Satana. (Chivumbulutso 12:7) Mikayeli ali ndi udindo waukulu kumwamba chifukwa amatchedwanso “mmodzi mwa akalonga aakulu” komanso “kalonga wamkulu.” (Danieli 10:13, 21; 12:1) Katswiri wina wa Baibulo dzina lake David E. Aune, ananena kuti mayinawa akusonyeza kuti Mikayeli ndi “mtsogoleri wa gulu la nkhondo la angelo.”

    Baibulo limatchulanso dzina lina la mngelo yemwe ali ndi udindo wotsogolera gulu la angelo. Limanena kuti, “Pa nthawi imene Ambuye Yesu adzaonekere kuchokera kumwamba limodzi ndi angelo ake amphamvu m’moto walawilawi, pa nthawi imeneyo adzabwezera chilango.” (2 Atesalonika 1:7, 8; Mateyu 16:27) Yesu “anapita kumwamba, ndipo angelo, maulamuliro, ndi mphamvu zinakhala pansi pake.”(1 Petulo 3:21, 22) Choncho n’zosamveka kuti Mulungu akonze zoti angelo ake oyera azitsogoleredwa ndi atsogoleri awiri osiyana, Yesu ndi Mikayeli. Pamenepatu, zikungosonyezeratu kuti mayina awiri onsewa, Yesu komanso Mikayeli akuimira munthu mmodzi.

  • Mikayeli ‘adzaimirira’ pa “nthawi ya masautso” imene sinakhalepo chiyambire. (Danieli 12:1) Nthawi zambiri buku la Danieli limagwiritsa ntchito mawu akuti ‘kuimirira’ likamafotokoza za mfumu yomwe yakonzeka kuti igwire ntchito inayake yofunika. (Danieli 11:2-4, 21) Yesu Khristu, yemwe amadziwika kuti “Mawu a Mulungu,” adzagwira ntchito monga “Mfumu ya mafumu” powononga adani a Mulungu komanso kuteteza anthu a Mulungu. (Chivumbulutso 19:11-16) Adzagwira ntchito imeneyi pa “chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko.”​—Mateyu 24:21, 42.

^ ndime 3 Baibulo limatchula anthu ena ndi mayina angapo. Mwachitsanzo Yakobo ankadziwikanso kuti Isiraeli, Petulo ankadziwikanso kuti Simoni ndipo Tadeyo ankadziwikanso kuti Yudasi.​—Genesis 49:1, 2; Mateyu 10:2, 3; Maliko 3:18; Machitidwe 1:13.