Pitani ku nkhani yake

Kodi Mkazi wa Kaini Anali Ndani?

Kodi Mkazi wa Kaini Anali Ndani?

Yankho la m’Baibulo

Kaini anali mwana woyamba pa ana onse a Adamu ndi Hava, ndipo anakwatira mmodzi wa azichemwali ake kapena m’bale wake wina. Tikutero chifukwa cha zimene Baibulo limanena zokhudza Kaini komanso anthu a m’banja lake.

Zokhudza Kaini komanso banja lake

  • Anthu onse anachokera kwa Adamu ndi Hava. Kuchokera mwa munthu mmodzi [Adamu], Mulungu “anapanga mtundu wonse wa anthu, kuti akhale padziko lonse lapansi.” (Machitidwe 17:26) Mkazi wa Adamu yemwe dzina lake ndi Hava, anakhala “mayi wa munthu aliyense wamoyo.” (Genesis 3:20) Choncho, Kaini ayenera kuti anakwatira mmodzi mwa ana amene Adamu ndi Hava anabereka.

  • Kaini komanso m’bale wake Abele anali woyamba pa ana amene Hava anabereka. (Genesis 4:1, 2) Kaini atathamangitsidwa chifukwa chopha m’bale wake, anadandaula kuti: “Aliyense wondipeza, adzandipha ndithu.” (Genesis 4:14) Kodi Kaini ankaopa ndani? Baibulo limati Adamu “anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.” (Genesis 5:4) N’zoonekeratu kuti ana ena a Adamu ndi Hava ndi amene akanapha Kaini.

  • Kale sizinali zodabwitsa munthu kukwatira m’bale wake. Mwachitsanzo Abulahamu, yemwe anali munthu wokhulupirika, anakwatira mchemwali wake amene anangosiyana naye mayi. (Genesis 20:12) Maukwati apachibale anayamba kuletsedwa mu Chilamulo cha Mose, chomwe chinaperekedwa zaka zambiri kuchokera pamene Kaini anafa. (Levitiko 18:9, 12, 13) Zikuoneka kuti ana amene ankabadwa kwa makolo omwe akwatirana pachibale, ankabadwa ndi zilema zochepa poyerekeza ndi ana a masiku ano.

  • Baibulo limafotokoza nkhani yokhudza Adamu, Hava, komanso banja lawo m’njira yosonyeza kuti nkhaniyi ndi yoona. Mndandanda wokhudza mibadwo imene inakhalapo kuyambira nthawi ya Adamu, sikuti umangopezeka m’buku la Genesis lokha lomwe linalembedwa ndi Mose, koma umapezekanso m’zomwe olemba mbiri Ezara komanso Luka analemba. (Genesis 5:3-5; 1 Mbiri 1:1-4; Luka 3:38) Olemba Baibulo amatchula nkhani yokhudza Kaini monga mbiri.—Aheberi 11:4; 1 Yohane 3:12; Yuda 11.