Kodi Mdyerekezi Angalamulire Zochita za Anthu?

Kodi Mdyerekezi Angalamulire Zochita za Anthu?

Yankho la m’Baibulo

 Zimene Mdyerekezi ndiponso ziwanda zimachita zimakhudza kwambiri zochita za anthu moti Baibulo limati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Baibulo limatiuza njira zimene Mdyerekezi amagwiritsa ntchito pofuna kusocheretsa anthu.

  •   Chinyengo. Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti ‘azilimbana ndi zochita zachinyengo za Mdyerekezi.’ (Aefeso 6:11) Imodzi mwa njira zake zachinyengo ndi yakuti amapusitsa anthu kuti aziona ngati atumiki ake ndi atumiki a Mulungu.—2 Akorinto 11:13-15.

  •   Kukhulupirira mizimu. Mdyerekezi amasocheretsa anthu pogwiritsa ntchito anthu olankhula ndi mizimu, olosera za m’tsogolo ndiponso anthu ochita zamatsenga kapena okhulupirira nyenyezi. (Deuteronomo 18:10-12) Zinthu zinanso zimene zimachititsa kuti munthu akodwe mumsampha wa ziwanda n’kugwiritsa ntchito mankhwala ogwirizana ndi mizimu, kugonekedwa tulo m’matsenga ndiponso kusinkhasinkha kogwirizana ndi mizimu.—Luka 11:24-26.

  •   Chipembedzo chonyenga. Zipembedzo zimene zimaphunzitsa anthu zinthu zabodza zimachititsa kuti anthuwo asamamvere Mulungu. (1 Akorinto 10:20) Baibulo limanena kuti zinthu zabodza zimene chipembedzo chonyenga chimaphunzitsa ndi “ziphunzitso za ziwanda.”—1 Timoteyo 4:1.

  •   Kugwidwa ndi ziwanda. M’Baibulo muli nkhani zosonyeza kuti mizimu yoipa imalamulira anthu ena. Nthawi zina ziwandazo zinkachititsa khungu anthuwo kapena kuwachititsa kuti asamalankhule, ngakhalenso kuwavulaza kumene.—Mateyu 12:22; Maliko 5:2-5.

Zimene mungachite kuti Mdyerekezi asamakulamulireni

 Musachite mantha kuti mwina ziwanda zingayambe kukulamulirani chifukwa Baibulo limasonyeza kuti mungathe kukana zoti Mdyerekezi azikulamulirani.

  •   Muzitha kuzindikira ndi kudziwa bwino ziwembu za Mdyerekezi n’cholinga choti asakukoleni.—2 Akorinto 2:11.

  •   Muziphunzira mfundo za m’Baibulo n’kumazigwiritsa ntchito. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuti musakodwe ndi misampha ya Mdyerekezi.—Aefeso 6:11-18.

  •   Mutaye kapena kuwotcha chinthu chilichonse chimene chikugwirizana ndi ziwanda. (Machitidwe 19:19) Zinthu zimenezi zingakhale nyimbo, mabuku, magazini, zithunzi ndiponso mavidiyo amene amalimbikitsa zamizimu.