Pitani ku nkhani yake

Kodi Mulungu Ali ndi Mayina Angati?

Kodi Mulungu Ali ndi Mayina Angati?

Yankho la m’Baibulo

 Mulungu ali ndi dzina limodzi lokha. M’chiheberi limalembedwa kuti יהוה ndipo m’Chichewa limadziwika kuti “Yehova.” a Kudzera mwa mneneri wake Yesaya, Yehova ananena kuti: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.” (Yesaya 42:8) Dzina limeneli limapezeka nthawi pafupifupi 7,000 m’mipukutu yakale ya Baibulo. Komanso dzinali limapezekamo nthawi zambiri kuposa mawu ena alionse ofotokoza za Mulungu kapenanso dzina la munthu wina aliyense wotchulidwa m’Baibulo. b

Kodi Mulungu ali ndi mayina enanso?

 Ngakhale kuti Baibulo limatchula kuti Mulungu ali ndi dzina limodzi lokha, limagwiritsanso ntchito mayina ena ambiri audindo komanso mawu ena ofotokoza za iye. Mayina audindo komanso mawu ofotokoza za Mulungu otsatirawa, akusonyeza mmene dzina lililonse likusonyezera mmene Yehova alili komanso umunthu wake.

Dzina Laudindo

Pomwe Likupezeka

Tanthauzo

Allah

(Palibe)

Mawu akuti Allah si dzina lenileni la Mulungu koma ndi mawu audindo a Chiarabu omwe amatanthauza kuti “Mulungu.” Ma Baibulo a m’Chiarabu komanso zilankhulo zina amagwiritsa ntchito mawu woti “Allah” kutanthauza “Mulungu.”

Wamphamvuyonse

Genesis 17:1

Ali ndi mphamvu zimene palibe wina aliyense yemwe angalimbane nazo. Mawu a Chiheberi akuti ʼEl Shad·daiʹ amatanthauza kuti “Mulungu Wamphamvuyonse” ndipo m’Baibulo amapezeka maulendo okwana 7.

Alefa ndi Omega

Chivumbulutso 1:8; 21:6; 22:13

Mawu amenewa amatanthauza kuti “woyamba ndi wotsiriza” kapena kuti “chiyambi ndi mapeto.” Zimenezi zikutanthauza kuti panalibenso Mulungu Wamphamvuyonse Yehova asanakhaleko ndipo sipadzakhalanso wina pambuyo pake. (Yesaya 43:10) Alefa ndi chilembo choyamba ndipo omega ndi chilembo chomaliza mu afabeti ya Chigiriki.

Wamasiku Ambiri

Danieli 7:9, 13, 22

Mulungu alibe chiyambi. Iye wakhala alipo kuyambira kalekale munthu aliyense komanso chinthu chilichonse zisanapangidwe.​—Salimo 90:2.

Mlengi

Yesaya 40:28

Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse.

Atate

Mateyu 6:9

Mulungu ndi amene amapereka moyo

Mulungu

Genesis 1:1

Woyenera kulambiridwa, Wamphamvu kwambiri. Mawu a Chiheberi akuti ʼElo·himʹ amanena za zinthu zambiri osati chimodzi ndipo zimenezi zikusonyeza ukulu, ulemerero komanso ubwino wa Yehova

Mulungu wa milungu

Deuteronomo 10:17

Mosiyana ndi “milungu yopanda phindu” imene anthu ena amailambira, Yehova ndi Mulungu wapamwamba kwambiri.​—Yesaya 2:8.

Mlangizi Wamkulu

Yesaya 30:20, 21

Amaphunzitsa komanso kupereka malangizo othandizadi.​—Yesaya 48:17, 18.

Wopanga Wamkulu

Salimo 149:2

Analenga zinthu zonse.​—Chivumbulutso 4:11.

Mulungu Wachimwemwe

1 Timoteyo 1:11

Ndi Mulungu wachisangalalo komanso chimwemwe.​—Salimo 104:31.

Wakumva Pemphero

Salimo 65:2

Amamvetsera ku pemphero lililonse loperekedwa kwa iye ndi chikhulupiriro.

Ine Ndine Yemwe Ndili Ine

Ekisodo 3:14, Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu

Amakhala chilichonse chimene akufuna n’cholinga choti akwaniritse cholinga chake. Mawu amenewa anawamasuliranso kuti “Ndidzakhala chilichonse chimene ndikufuna” kapena kuti “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.” (The Emphasised Bible, lolembedwa ndi J. B. Rotherham komanso Baibulo la Dziko Latsopano) Zimenezi zimathandiza kufotokoza tanthauzo la dzina la Mulungu lakuti, Yehova, limene lili mu vesi lotsatira.​—Ekisodo 3:15.

Nsanje

Ekisodo 34:14

Amafuna kuti iye yekha ndi amene azilambiridwa. Mawu amenewa anamasuliridwanso kuti “safuna kuti aliyense azipikisana naye” komanso kuti “amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.”​—Baibulo la Mawu a Mulungu komanso la New World Translation Revised 2013

Mfumu yamuyaya

Chivumbulutso 15:3

Ulamuliro wake ulibe chiyambi komanso mapeto.

Ambuye

Salimo 135:5

Mwiniwake kapena kuti mbuye. Mu Chiheberi mawuwa ndi ʼA·dhohnʹ komanso ʼAdho·nimʹ.

Yehova Wamakamu

Yesaya 1:9, Aroma 9:29

Yehova ndi mtsogoleri wa khamu lalikulu la angelo. Dzina la udindo lakuti “Yehova Wamakamu” lingamasuliridwenso kuti “Mbuye wa magulu a nkhondo akumwamba.”—Aroma 9:29, Baibulo la NET, mawu a m’munsi.

Wam’mwambamwamba

Salimo 47:2

Ndi wamkulu kwambiri m’chilengedwe chonse.

Woyera Koposa

Miyambo 9:10

Makhalidwe ake ndi oyera kwambiri kuposa munthu wina aliyense.

Woumba

Yesaya 64:8

Ali ndi ulamuliro pa munthu aliyense komanso mitundu yonse ya anthu monga mmene woumba mbiya alili ndi ulamuliro pa dongo.​—Aroma 9:20, 21.

Wowombola

Yesaya 41:14

Amaombola kapena kugulanso anthu ku uchimo ndi imfa pogwiritsa ntchito nsembe ya dipo ya Yesu Khristu.​—Yohane 3:16.

Thanthwe

Salimo 18:2, 46

Ndi malo achitetezo komanso chipulumutso.

Mpulumutsi

Yesaya 45:21

Amapulumutsa anthu ku zinthu zoopsa kapena zimene zingawawononge.

M’busa

Salimo 23:1

Amasamalira anthu amene amamutumikira.

Ambuye Wamkulu Koposa

Genesis 15:2

Ali ndi ulamuliro wopanda malire ndipo mu Chiheberi amagwiritsa ntchito mawu oti ʼAdho·naiʹ.

Wamkulukulu

Danieli 7:18, 27

Yehova ndi wolamulira wamkulu mu chilengedwe chonse.

Mayina a Malo M’malemba Achiheberi

 Mayina ena a malo otchulidwa m’Baibulo ali ndi dzina la Mulungu lakuti Yehova koma sikuti mayinawa ndi mayina ena a Mulungu.

Dzina la malo

Pomwe Likupezeka

Tanthauzo

Yehova-yire

Genesis 22:13, 14

“Yehova Adzapereka Zofunika.”

Yehova-nisi

Ekisodo 17:15

“Yehova Ndiye Mlongoti Womwe Ndi Chizindikiro Changa,” kapena “Mbendera yanga.” (Baibulo la Today’s New International Version) Yehova ndi Mulungu amene anthu omwe amamutumikira angadalire kuti awateteze komanso kuwathandiza.​—Ekisodo 17:13-16.

Yehova-salomu

Oweruza 6:23, 24

“Yehova Ndi Mtendere.”

Yehova-sama

Ezekieli 48:35, American Standard Version, mawu a m’munsi

“Yehova Ali Kumeneko.”

N’chifukwa chiyani tiyenera kudziwa komanso kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu?

  •   Mulungu amaona kuti dzina lake lakuti Yehova ndi lofunika kwambiri ndipo n’chifukwa chake analilemba m’Baibulo maulendo ambiri.​—Malaki 1:11.

  •   Mobwerezabwereza, Yesu yemwe ndi Mwana wa Mulungu, anatsindika kufunika kwa dzina la Mulungu. Mwachitsanzo, iye anapemphera kwa Yehova kuti: “Dzina lanu liyeretsedwe.”​—Mateyu 6:9; Yohane 17:6.

  •   Anthu amene amadziwa komanso kugwiritsa ntchito dzina la Yehova amakhala akuchita zinthu zoyenera zomwe zingawathandize kuti akhale naye paubwenzi. (Salimo 9:10; Malaki 3:16) Anthu amene ali paubwenzi ndi Yehova amapindula ndi lonjezo lake lakuti: “Popeza wasonyeza kuti amandikonda, Inenso ndidzamupulumutsa. Ndidzamuteteza chifukwa wadziwa dzina langa”Salimo 91:14.

  •   Baibulo limavomereza kuti: “Ilipo yotchedwa milungu, kaya kumwamba kapena padziko lapansi, ndipo n’zoona ilipodi ‘milungu’ yambiri ndi ‘ambuye’ ambiri” (1 Akorinto 8:5, 6) Komabe limanena momveka bwino kuti dzina la Mulungu yekhayo amene ndi woona ndilo Yehova.​—Salimo 83:18.

a Akatswiri ena a Chiheberi amakonda kugwiritsa ntchito “Yahweh” potchula dzina la Mulungu.

b Dzina lachidule la Mulungu lakuti “Ya” lomwe lilinso m’mawu akuti “Aleluya,” limapezeka nthawi pafupifupi 50 m’Baibulo. Mawu akuti “Aleluya” amatanthauza kuti “Tamandani Ya.”​—Chivumbulutso 19:1; Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu.