Pitani ku nkhani yake

Kodi Mariya Ndi Amayi a Mulungu?

Kodi Mariya Ndi Amayi a Mulungu?

Yankho la m’Babulo

 Baibulo silinena kuti Mariya ndi amayi a Mulungu. Komanso silifotokoza kuti Akhristu azipembedza Mariya kapena kumupatsa ulemu wapadera. a Taganizirani izi:

  •   Mariya sanafotokozepo zoti iye ndi amayi a Mulungu. Baibulo limanena kuti iye anabereka “Mwana wa Mulungu” b osati Mulungu weniweniyo.​—Maliko 1:1; Luka 1:32.

  • Yesu Khristu sananene kuti Mariya anali a mayi a Mulungu komanso kuti azipatsidwa ulemu wapadera. Ndipotu nthawi ina, mayi wina ananena kuti Mariya anali wodala chifukwa anabereka Yesu. Koma Yesu anamuuza kuti: “Ayi, m’malomwake, odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.”​—Luka 11:27, 28.

  •   Mawu akuti “Mayi a Mulungu” komanso akuti “Theotokos” kapena kuti “Wobereka Mulungu,” sapezeka m’Baibulo.

  •   M’Baibulo mawu akuti “Mfumukazi Yakumwamba,” sanena za Mariya. Koma amanena za mulungu wamkazi yemwe Aisiraeli omwe anasiya kutumikira Yehova ankamulambira. (Yeremiya 44:15-19) N’kutheka kuti Mfumukazi Yakumwambayi inali mulungu wamkazi wa ku Babulo yemwe ankadziwika ndi dzina lakuti Ishitara kapena Asitaroti.

  •   Akhristu oyambirira sankalambira Mariya kapena kumupatsa ulemu wapadera. Katswiri wina wolemba mbiri yakale ananena kuti Akhristu oyambirira “ayenera kuti ankakana kupembedza Mariya ndipo sankamupatsa ulemu wapadera chifukwa anthu ena akanayamba kuganiza kuti amalambira mulungu wamkazi.”​—In Quest of the Jewish Mary.

  •   Baibulo limanena kuti Mulungu anakhalapo kuyambira kalekale. (Salimo 90:1, 2; Yesaya 40:28) Ndiye chifukwa choti Mulungu alibe chiyambi, sizingatheke kuti akhale ndi mayi ake. Kuwonjezera pamenepo Baibulo limanena kuti Mulungu sangakwane kumwamba. Ndiye kodi zikanakhala zotheka kuti akwane m’mimba mwa Mariya?​—1 Mafumu 8:27.

Mariya ndi Mayi ake a Yesu osati “Mayi a Mulungu”

 Mariya anali Myuda ndipo anabadwira mfuko la Mfumu Davide. (Luka 3:23-31) Mulungu ankamukonda kwambiri chifukwa cha chikhulupiriro chake. (Luka 1:28) Ndipo anamusankha kuti akhale mayi ake a Yesu. (Luka 1:31, 35) Patapita nthawi, Mariya ndi mwamuna wake Yosefe, anaberekanso ana ena.​—Maliko 6:3.

 Ngakhale kuti Baibulo limafotokoza kuti Mariya anadzakhala wophunzira wa Yesu, silifotokoza zambiri zokhudza iyeyo.​—Machitidwe 1:14.

a Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti Mariya ndi amayi a Mulungu. Zimanena kuti Mariya ndi “Mfumukazi Yakumwamba” kapena kuti Theotokos, mawu achigiriki omwe amatanthauza kuti “wobereka Mulungu.”

b Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu